Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

 INDONESIA

Ntchito Yolalikira Inafika Mpaka ku Zilumba Zakum’mawa

Ntchito Yolalikira Inafika Mpaka ku Zilumba Zakum’mawa

Mu 1953, M’bale Peter Vanderhaegen anatumizidwa kuti akakhale woyang’anira dera ku Indonesia. Dera lake linali dziko lonse la Indonesia ndipo linali lalikulu makilomita 5,100 kuchoka kum’mawa kupita kumadzulo komanso makilomita 1,800 kuchokera kumpoto kupita kum’mwera. Pamene m’baleyu ankayendera derali anakumana ndi mavuto osiyanasiyana.

M’bale Peter Vanderhaegen

Mu 1954, M’bale Vanderhaegen anapita m’chigawo chakum’mawa kwa Indonesia komwe kuli zipembedzo zambiri. Anafika kuchilumba cha Bali komwe kuli Ahindu ambiri, kuzilumba za Lombok ndi Sumbawa komwe kuli Asilamu ambiri komanso kuchilumba cha Flores komwe ambiri ndi Akatolika. Kenako anafikanso kuzilumba za Sumba, Alor ndi Timor, komwe kuli zipembedzo zachipulotesitanti. M’baleyu  ankayenda paboti ndipo analalikira kwa nthawi yochepa pazilumba zingapo asanafike mumzinda wa Kupang, womwe ndi likulu la chilumba cha Timor. M’bale Vanderhaegen ananena kuti: “Ndinalalikira pachilumba cha Timor kwa milungu iwiri. Ngakhale kuti kunkabwera mvula yambiri, ndinagawira mabuku onse amene ndinali nawo. Anthu 34 analembetsa kuti akufuna kuti azilandira mabuku mwezi ndi mwezi komanso ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu angapo.” Apainiya apadera anapitiriza kuphunzira ndi anthu amene anayamba kuphunzira ndi m’baleyu ndipo anakhazikitsa mpingo ku Kupang. Kenako uthenga wabwino unafikanso kuzilumba za Rotè, Alor, Sumba ndi Flores.

Atsogoleri achipembedzo chachipulotesitanti ku Kupang ataona kuti anthu a m’chipembedzo chawo ayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova, anakwiya kwambiri. M’busa wina anauza a Thomas Tubulau kuti asiye kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. A Tubulau anali ndi dzanja limodzi ndipo ankagwira ntchito yokhoma zidebe. M’busa uja anawauzanso kuti ngati sasiya kuuza ena zimene ankaphunzira, aona zakuda. Koma a Tubulau anayankha molimba mtima kuti: “Mkhristu weniweni sanganene zimene mwanenazi. Sindidzabweranso kutchalitchi kwanuko.” A Tubulau anayamba kulalikira mwakhama ndipo mwana wawo wamkazi anakhala mpainiya wapadera.

Komabe atsogoleri achipembedzo ku Timor ankafunitsitsa kuthetseratu gulu la Mboni za Yehova. Mu 1961, atsogoleri achipembedzowa anakakamiza akuluakulu a nthambi yoona za zipembedzo komanso asilikali a m’derali kuti aletse ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Choncho abale anasintha njira yolalikirira. Anayamba kulalikira kwa anthu m’misika, pa zitsime, kwa asodzi omwe ankawapeza m’mbali mwa nyanja komanso kwa anthu amene ankawapeza akulambula manda. Patadutsa mwezi umodzi, akuluakulu a asilikali anasintha maganizo ndipo analengeza pa wailesi kuti palibe chipembedzo choletsedwa ku Timor. Koma akuluakulu a ku nthambi yoona za zipembedzo sanasinthe maganizo moti ankanenabe kuti ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba idakali yoletsedwa.  Abale atamva zimenezi, anapempha akuluakuluwo kuti alembe kalata yotsimikizira kuti ntchito ya a Mboni ndi yoletsedwa koma iwo anakana kulemba kalatayo. Pamenepo abale anapitiriza kugwira ntchito yawo yolalikira kunyumba ndi nyumba mwaufulu.

M’chaka cha 1962, mabanja awiri omwe anali amishonale anafika m’dziko la Papua. Mayina awo anali M’bale Piet ndi Mlongo Nell de Jager komanso M’bale Hans ndi Mlongo Susie van Vuure. Amishonalewa atayamba kulalikira, atsogoleri achipembedzo anayamba kutsutsa ntchito yawo moti tsiku lina atsogoleri atatu anakumana ndi amishonalewa n’kuwauza kuti akalalikire kwina. Iwo analemba m’manyuzipepala, analengeza pawailesi komanso ankalengeza m’matchalitchi awo kuti a Mboni za Yehova ndi anthu amene amatsutsana ndi boma. Ankanyengerera, kuopseza kapenanso kupereka ziphuphu kwa anthu a m’chipembedzo chawo n’cholinga choti asiye kuphunzira Baibulo ndi amishonalewa. Anakakamizanso mafumu kuti aziletsa ntchito yathu yolalikira.

Koma zinthu zinasintha mfumu ina itapempha amishonalewa kuti ayankhule kwa anthu a m’mudzi mwake. M’bale van Vuure ananena kuti: “Mfumuyi itasonkhanitsa anthu, ineyo ndi M’bale de Jager tinakamba nkhani ziwiri zachidule ndipo tinafotokoza zimene timachita tikamalalikira. Kenako, azikazi athu anachita chitsanzo chosonyeza zimene timachita tikafika pakhomo la munthu. Mfumuyi pamodzi ndi anthu ake, anasangalala kwambiri moti anatilola kuti tipitirize kulalikira.”

Nkhani zosangalatsa ngati zimenezi zinkachitika kawirikawiri. Atsogoleri a matchalitchi ndi amene ankatsutsa ntchito yathu, koma Asilamu ambiri amene ankakhala m’derali sankachita zimenezi ndipo ndi zimene zikuchitikabe mpaka pano.

‘Anawatengera kwa Abwanamkubwa . . . Kuti Ukhale Umboni’

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.” (Mat. 10:18) Zimenezi ndi zomwe zakhala zikuchitika m’dziko la Indonesia.

 M’chaka cha 1960, katswiri wina wa zachipembedzo ku Jakarta analemba buku lomwe linanena kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu abodza. Bukuli linachititsa kuti atsogoleri azipembedzo azilimbana kwambiri ndi a Mboni. Mwachitsanzo, m’tauni ina, atsogoleri achipembedzo analemba kalata yopita ku nthambi yoona za zipembedzo. Kalatayi inali yoimba mlandu a Mboni za Yehova kuti akusokoneza anthu a m’zipembedzo zawo. Akuluakuluwo anaitana abale kuti akayankhepo pa mlanduwu. Abalewo anawafotokozera zoona zenizeni komanso anapezerapo mwayi wowalalikira. Mtsogoleri wina wachipembedzo anauza mnzake kuti: “Asiyeni a Mboni azilalikira. Mwina angachangamutse Apulotesitanti atulowa.”

Akutsitsa mabuku a Paradise mu 1963

Mu 1964, atsogoleri achipembedzo a ku Papua anapempha komiti yoona za zipembedzo ku nyumba ya malamulo kuti  aike lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Koma abale ku ofesi ya nthambi anapempha kuti akumane ndi komitiyi kuti afotokoze mbali yawo. M’bale Tagor Hutasoit ananena kuti: “Tinayankhula ndi anthu a m’komitiyi pafupifupi ola limodzi ndipo tinawafotokozera momveka bwino zokhudza ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo. Koma munthu wina wandale yemwe anali m’tchalitchi chachipulotesitanti anatiimba mlandu wabodza woti timasokoneza anthu a matchalitchi ena ku Papua. Komabe anthu a m’komitiyo, amene anali Asilamu ankatimvera chisoni. Iwo anatiuza kuti: ‘Malamulo a dziko lino amavomereza kuti anthu azipemphera mwaufulu, choncho inuyo muli ndi ufulu wolalikira.’” Msonkhanowu utatha, munthu wina amene anali ndi udindo waukulu ku Papua, analengeza kuti: “Boma latsopano . . . lipitirizabe kupereka ufulu wopembedza kwa munthu aliyense, komanso ku zipembedzo zatsopano.”