• CHAKA CHOBADWA 1928

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1957

  • MBIRI YAKE Mlongo amene anathandiza mwamuna wake mwaluso kwambiri kuti aphunzire choonadi ngakhale kuti poyamba ankamutsutsa.—Yofotokozedwa ndi mwana wake wamwamuna, dzina lake Mario Koetin.

MAYI anga anali munthu wokoma mtima, wochezeka komanso ankakonda kuwerenga Baibulo. Anayamba kuphunzira Baibulo atakumana ndi Mlongo Gertrud Ott, yemwe anali mmishonale, mumzinda wa Manado ku North Sulawesi ndipo kenako anabatizidwa. Koma bambo anga a Erwin, omwe ankagwira ntchito ku banki ndipo kenako anagwira ntchito kumsika wogulitsa makampani ku Jakarta, ankatsutsa kwambiri zimene mayi anga ankakhulupirira.

Tsiku lina, bambo anga anawaopseza kwambiri mayi anga.

Bambo anga atakwiya kwambiri ananena kuti: “Usankhepo chimodzi, pakati pa chipembedzo chakocho kapena banja.”

Mayi anga anangokhala chete n’kumaganizira zimene bambo ananenazi. Kenako anawayankha kuti: “Ndikufuna zonse. Ndikufuna kukhala pa banja ndi inuyo komanso kuti ndizitumikira Yehova.”

Bambo anga anasowa chonena ndipo mkwiyo wonse unathera pomwepo.

Patapita nthawi, bambo anayamba kuchita zinthu mokoma mtima ndi amayi. Iwo anayamba kulemekeza maganizo awo komanso kuwakonda kwambiri.

 Komabe mayi anga ankafunitsitsa kuti bambo anga aphunzire choonadi. Ataipempherera nkhaniyi, anakumbukira kuti bambo amakonda kuphunzira ziyankhulo. Choncho anaganiza zomaika timapepala tokhala ndi mavesi a m’Baibulo achingelezi pamalo osiyanasiyana m’nyumbamo kuti azitiona. Ankawauza kuti akuchita zimenezo n’cholinga choti aphunzire Chingelezi. Mayi ankadziwanso kuti bambo ankakonda kumvetsera munthu akamakamba nkhani pagulu. Choncho ankawapempha kuti aziwamvetsera akamakonzekera nkhani yoti akakambe m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndipo iwo anavomera. Komanso popeza bambo ankakonda kuchereza alendo, tsiku lina mayi anawapempha kuti woyang’anira dera akamadzachezera mpingo wathu, azidzagonera kunyumba kwathu ndipo anavomera. Mayi ankadziwanso kuti bambo amakonda kwambiri banja lawo, choncho anawapempha ngati angakonde kuti adzapite nafe limodzi kumisonkhano yathu. Apanso anavomera.

Zimene mayi anachitazi zinathandiza kuti pang’ono ndi pang’ono bambo asinthe. Kenako banja lathu litasamukira ku England, bambo anayamba kupita kumisonkhano. Kumisonkhanoko anakumana ndi M’bale John Barr, yemwe anadzakhala wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo anakhala mnzawo. Bambo anga anabatizidwa m’chaka chimenecho, ndipo mayi anasangalala kwambiri. Kuyambira nthawi imeneyi, bambo ankakonda kwambiri amayi.

Mayi anga anali munthu wabwino kwambiri chifukwa ankakonda komanso kulemekeza bambo anga. Ankakondanso kwambiri Yehova moti anthu ambiri ankawaona kuti ndi munthu wabwino

Anzathu ena amanena kuti mayi anali ngati Lidiya wa m’nthawi ya atumwi yemwe anali wochereza alendo. (Mac. 16:14, 15) Koma ine ndimaona kuti mayi ankachita zinthu ngati Sara, yemwe ankagonjera kwambiri mwamuna wake, Abulahamu. (1 Pet. 3:4-6) Ndimaona kuti mayi anga anali munthu wabwino kwambiri chifukwa ankakonda komanso kulemekeza bambo anga. Ankakondanso kwambiri Yehova moti anthu ambiri ankawaona kuti ndi munthu wabwino. Makhalidwe awo abwinowa ndi amene anathandiza bambo kuphunzira choonadi. Mayi anga analidi ngati Sara weniweni.