Maofesi omwe ali pansanjika ya nambala 31

Mu 2008, chiwerengero cha ofalitsa m’dziko la Indonesia chinafika 21,699. Zimenezi zinachititsa kuti pafunike abale ndi alongo ambiri otumikira pa Beteli kuti ntchito yosamalira ofalitsawa iziyenda bwino. Choncho panafunika kuti amangenso nyumba zogona komanso maofesi a abale ndi alongo amenewa. Koma chifukwa chakuti maofesi omwe ankagwiritsidwa ntchito pa nthawiyi anamangidwa pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa, anali  kutali kwambiri ndi mzinda wa Jakarta. Choncho abalewa anaona kuti ndi bwino kuti maofesiwa akhale pafupi ndi mzindawu. Apa, zinali zoonekeratu kuti pankafunika maofesi atsopano.

Patapita zaka ziwiri, abale anagula maofesi ena omwe ali pansanjika ya nambala 31 m’nyumba ina yansanjika 42, yomwe ili pakatikati pa mzinda wa Jakarta. Maofesiwa anali osiyana ndi a poyamba aja chifukwa anamangidwa mwamakono. Kenako abale anagula nsanjika zina 12 za nyumba ina pafupi ndi maofesiwa kuti muzikhala abale 80 omwe akutumikira pa Beteli. Anagulanso nyumba ina yansanjika 5 kuti muzigona abale ogwira ntchito zosiyanasiyana pa Beteli.

Nyumba zogonamo anthu otumikira pa Beteli zomwe zili m’nsanjika 12

Abale ogwira ntchito ya zomangamanga ochokera kumayiko osiyanasiyana anagwira ntchito yokonzanso maofesi komanso nyumbazi limodzi ndi kampani ina ya zomangamanga ya m’dzikoli. M’bale Darren Berg amene ankayang’anira ntchitoyo, anati: “Yehova anapitirizabe kutithandiza pamene tinkakumana ndi zinthu zomwe zinkaoneka ngati zikhoza kulepheretsa ntchito yathu. Mwachitsanzo, tinkafuna kuika makina atsopano oti azisefa madzi omwe tawagwiritsa ntchito. Koma akuluakulu aboma anakana kutipatsa chilolezo chifukwa sankadziwa mmene njira yatsopanoyi imagwirira ntchito. Kenako m’bale wina yemwe ndi injiniya anapita ndi nkhaniyi kwa mkulu wina waboma. Mkulu wa bomayo anatipatsa chilolezo nthawi yomweyo ndipo ananena kuti anachita zimenezi chifukwa anakhulupirira zimene m’baleyo anamufotokozera.”

“Panopa tili pamalo oonekera kusiyana ndi kale ndipo anthu ayamba kudziwa a Mboni za Yehova”

Mwambo wotsegulira maofesi atsopanowa unachitika pa 14 February, 2015. M’bale Anthony Morris III wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani yotsegulira maofesiwa. Kenako M’bale Vincent Witanto Ipikkusuma, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi, ananena kuti: “N’zosangalatsa kuti panopa tili mkatikati mwa tauni yotchuka yomwe mulinso makampani akuluakulu ku Indonesia kuno. Panopa tili pamalo oonekera kusiyana ndi kale ndipo anthu ayamba kudziwa a Mboni za Yehova.”

Abale a m’Komiti ya Nthambi kuchokera kumanzere kupita kumanja: Budi Sentosa Lim, Vincent Witanto Ipikkusuma, Lothar Mihank, Hideyuki Motoi

 “Kulalikira M’dziko la Indonesia N’kosangalatsa Kwambiri”

M’zaka zaposachedwapa, abale ndi alongo ochokera kumayiko osiyanasiyana anasamukira m’dziko la Indonesia. M’bale Lothar Mihank yemwe ali m’komiti ya nthambi m’dzikoli ananena kuti: “Abale ndi alongo amene amasamukira m’mayiko ena amene kulibe ofalitsa ambiri ngati lathuli, amathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira. Iwo amakhala odziwa bwino ntchito yolalikira komanso okhwima mwauzimu. Zimenezi zimathandiza abale ndi alongo kuti aziphunzitsa mogwira mtima ndiponso zimalimbikitsa ubale wapadziko lonse.” Koma kodi n’chiyani chimachititsa abalewa kusamukira kumayiko ena? Nanga kodi zinthu zimawayendera bwanji akapita kumayiko amenewa? Tiyeni tione zimene ena mwa abalewa ananena.

Abale ndi Alongo Otumikira M’mayiko Amene Kulibe Ofalitsa Ambiri

1. Dan ndi Janine Moore

2. Stuart ndi Mandy Williams

3. Jason ndi Casey Gibbs

4. Mari (kutsogolo chakumanja) ndi Takahiro Akiyama (kumbuyo chakumanja)

M’bale Jason ndi Mlongo Casey Gibbs omwe anachokera ku United States anati: “Tisanabwere kuno tinawerenga mu Buku Lapachaka kuti dziko la Indonesia ndi limodzi mwa mayiko omwe ali ndi ofalitsa ochepa poyerekeza ndi anthu okhala m’dzikoli. Anzathu enanso omwe anali atabwera kale kuno, anatiuza kuti kuli anthu ambiri amene akufuna kuphunzira choonadi. Choncho tinaimba foni ku ofesi ya nthambi ndipo anatiuza kuti tikayambe utumiki wathu pachilumba cha Bali. Pa nthawiyo m’deralo munali mutayamba kupezeka anthu ambiri oyankhula Chingelezi moti  zinali zosavuta kulalikira. Poyamba tinali ndi maganizo oti tidzangokhalako chaka chimodzi chokha basi koma panopa takhala zaka zitatu. Anthu ambiri omwe timawalalikira sanayambe amvapo zokhudza Mboni za Yehova. Kunena zoona, Yehova wadalitsa kwambiri utumiki wathuwu.”

M’bale Stuart ndi Mlongo Mandy Williams ali ndi zaka pafupifupi 50 ndipo anachokera ku Australia. Iwo anati: “Tinkafunitsitsa kulalikira anthu omwe anali ndi njala ya choonadi. Choncho tinaganiza zosamukira m’dziko la Indonesia. Mumzinda uno wa Malang, ku East Java, timakumana ndi anthu ophunzira pa yunivesite ndipo ambiri amayankhula Chingelezi. Anthuwa amamvetsera mwachidwi uthenga wabwino ndipo amakonda kwambiri webusaiti yathu ya jw.org. Kulalikira kuno n’kosangalatsa kwambiri.”

M’bale Takahiro ndi Mlongo Mari Akiyama akutumikira monga apainiya mumzinda wa Yogyakarta pachilumba cha Java. Iwo anati: “Kunoko timalalikira mtima uli m’malo kusiyana ndi mmene zimakhalira tikakhala kwathu ku Japan. Anthu ake ndi okoma mtima komanso aulemu. Anthu ambiri, makamaka achinyamata, amakhala ndi mafunso osiyanasiyana okhudza zipembedzo zina. Tsiku lina tikulalikira m’malo opezeka anthu ambiri, tinagawira magazini pafupifupi 2,600 m’maola 5 okha.”

M’bale Dan ndi Mlongo Janine Moore omwe ali ndi zaka pafupifupi 60 ananena kuti: “Tikamalalikira, anthu amabwera pamene tili kuti adzamvetsere uthenga wathu. Tikamwetulira munthu, nayenso amatimwetulira ndipo amabwera kuti adzamve kuti pali zotani. Tikawerenga lemba lina la m’Baibulo anthu ena amafunsa kuti, ‘Ndi vesi lanji limene mwawerengalo? Ndikufuna kuti ndilembe.’ Anthu ambiri amasangalala ndi uthenga wa m’Baibulo. Panopa patha chaka chimodzi chokha chibwerereni kuno. Timangodandaula kuti tinadziwa mochedwa kuti kuno n’kosangalatsa chonchi chifukwa bwenzi titabwera kalekale. Tinkafunitsitsa gawo la anthu ofuna kudziwa choonadi ngati limeneli, ndipo talipeza.”

M’bale Misja ndi Mlongo Kristina Beerens anapita kukatumikira m’dziko la Indonesia ngati amishonale mu 2009 koma panopa ndi oyang’anira dera. Iwo anati: “Anthu ambiri a pachilumba cha Madura ku East Java ndi Asilamu ndipo amasunga kwambiri  chikhalidwe chawo komabe amamvetsera uthenga wa Ufumu. Ambiri akationa amaimitsa magalimoto awo n’kutipempha kuti tiwapatse magazini. Amanena kuti, ‘Ndine Msilamu koma ndimakonda kuwerenga magazini anu. Kodi ndingawatengerekonso anzanga?’ Kunena zoona, kulalikira m’dziko la Indonesia n’kosangalatsa kwambiri.”

M’munda Mwayera Ndipo M’mofunika Kukolola

Mu 1931, pamene M’bale Frank Rice anafika mumzinda wa Jakarta, chiwerengero cha anthu okhala m’dziko la Indonesia chinali 60,000,000. Koma panopa chiwerengerochi chatsala pang’ono kukwana 260,000,000. Popeza m’dzikoli muli anthu ambiri, dziko la Indonesia ndi la nambala 4 pa mayiko amene ali ndi anthu ambiri padziko lonse lapansi.

 Chiwerengero cha Mboni za Yehova m’dzikoli nachonso chawonjezereka. Mu 1946, kunali ofalitsa 10 okha omwe anayamba kulalikira uthenga wabwino nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha. Koma masiku ano, m’dzikoli muli ofalitsa oposa 26,000. Umenewu ndi umboni woti Yehova wakhala akudalitsa ntchito yathu. Komanso poona anthu 55,864 omwe anapezeka pa Chikumbutso cha chaka cha 2015, n’zosakayikitsa kuti chiwerengero cha ofalitsa chipitiriza kuwonjezereka m’dziko la Indonesia.

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Atumiki a Yehova ku Indonesia akusonyeza kuti mawu amenewa ndi oona. Iwo akugwira mwakhama ntchito yolalikira pothandiza kuti dzina la Yehova lilemekezedwe m’dzikoli.—Yes. 24:15.