• CHAKA CHOBADWA 1957

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1997

  • MBIRI YAKE Anabwerera kumudzi wakwawo womwe uli pachilumba cha Nias ndipo anathandiza kuti Nyumba ya Ufumu imangidwe m’mudziwo.

MPINGO wathu uli m’dera la Tugala Oyo ndipo muli ofalitsa ochepa. M’chaka cha 2013, abale ndi alongo a mumpingo wathu anasangalala atamva chilengezo choti atimangira Nyumba ya Ufumu. Nawonso akuluakulu a m’derali anasangalala moti anatipatsa chilolezo chomanga nyumbayo. Komanso anthu 60 okhala m’derali anasaina chikalata chovomereza kuti timange Nyumba ya Ufumuyi. Munthu wina anati: “Ngati mukufuna anthu 200 oti asaine chikalatachi ndikhoza kukupezerani msangamsanga.”

Abale awiri odziwa bwino ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi amene ankayang’anira ntchitoyi ndipo inamalizidwa mu November 2014. Sitinkayembekezera kuti mpingo wathu ungakhale ndi malo abwino ngati amenewa ochitira misonkhano. Ndithudi, Yehova anatichitira zinthu zoposa zimene tinkayembekezera.