Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Ntchito Yolalikira Inabala Zipatso ku West Java

Theodorus Ratu

Ntchito Yolalikira Inabala Zipatso ku West Java

M’chaka cha 1933, M’bale Frank Rice anapempha M’bale Theodorus Ratu, yemwe anali nzika ya ku North Sulawesi, kuti adzamuthandize ntchito zina pa ofesi yolandirira mabuku ku Jakarta. M’bale Ratu ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi komanso ndinayamba kulalikira ndi M’bale Rice. Kenako ndinayamba kuyenda ndi M’bale Bill Hunter ndipo tinalalikira limodzi pachilumba cha Java. Ndinayendanso ndi kagulu ka abale amene ankakalalikira ku Sumatra omwe ankayenda pasitima yotchedwa Lightbearer.” M’bale Ratu anali munthu woyamba kuphunzira Baibulo ku Indonesia. Iye anachita upainiya kwa zaka zambiri pachilumba cha Java, North Sulawesi komanso Sumatra.

Chaka chotsatira, M’bale Hunter analalikira Felix Tan yemwe pa nthawiyo anali pasukulu mumzinda wa Jakarta. Anamugawira kabuku kakuti Kodi Akufa Ali Kuti? Felix atabwerera kwawo ku Bandung, anaonetsa mng’ono wake dzina lake Dodo kabuku kaja. Anyamatawa anadabwa kwambiri atawerenga m’kabukuka kuti Adamu, yemwe anali munthu woyamba kulengedwa, analibe mzimu womwe suufa. (Gen. 2:7) Mfundoyi inawachititsa chidwi kwambiri moti anayamba kufuna kudziwa zambiri. Choncho anapita kumalo osiyanasiyana ogulitsira mabuku ku Bandung kukafufuza  mabuku ofalitsidwa ndi a Mboni. Anayambanso kuuza achibale awo zimene ankawerenga m’mabukuwa. Atawerenga mabuku komanso timabuku tonse timene anapeza, analemba kalata yopempha mabuku ku ofesi yathu ya ku Jakarta. Anyamatawa anasangalala kwambiri M’bale Frank Rice atabwera kudzawaona komanso kudzawapatsa mabuku atsopano.

Banja la a Tan

M’bale Rice atabwerera ku Jakarta, M’bale Clem ndi mlongo Jean Deschamp, omwe anali atangokwatirana kumene, anapita ku Bandung komwe anakakhalako masiku 15. Felix ananena kuti: “M’bale Deschamp anandifunsa ineyo ndi anthu a m’banja lathu ngati tinkafuna kubatizidwa. Choncho anthu 4 a m’banja lathu, omwe ndi Dodo, m’chemwali wanga wamng’ono Josephine yemwe amadziwikanso kuti Pin Nio, mayi anga a Kang Nio ndi ineyo, tinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu.” * Anthuwa atabatizidwa anayamba ulendo wamasiku 9  wokalalikira pamodzi ndi banja la a Deschamp. M’bale Deschamp anawaphunzitsa mmene angalalikirire pogwiritsa ntchito khadi lomwe linkakhala ndi uthenga wachidule wa m’Baibulo m’ziyankhulo zitatu. Pasanapite nthawi, kagulu ka ku Bandung kanakula n’kukhala mpingo. Mpingowu ndi umene unali wachiwiri kukhazikitsidwa m’dziko la Indonesia.

Nkhani ya Chipewa cha Papa Inavuta

Atsogoleri a matchalitchi omwe amati ndi achikhristu anadabwa kwambiri atazindikira kuti ntchito yathu yolalikira ikuyenda bwino. Zimenezi zinachititsa kuti atsogoleriwa komanso anthu omwe ankawatuma alembe nkhani m’nyuzipepala, zonyoza a Mboni za Yehova ndiponso zimene amakhulupirira. Zimene analembazo zinachititsa kuti a nthambi yoona za ufulu wa zipembedzo aitanitse M’bale Frank Rice kuti akamufunse mafunso. Atakhutira ndi zimene m’baleyu anawayankha, akuluakulu a bomawa analola kuti abalewo apitirize kugwira ntchito yawo. *

Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, akuluakulu a boma ankavomereza ntchito yolalikira ndipo sankachita chidwi ndi zoti ntchitoyo ikuyenda bwanji. Koma chipani cha Nazi cha ku Germany chitayamba kulamulira ku Europe, akuluakulu a boma makamaka omwe anali odzipereka m’chipembedzo cha Katolika, anayamba kupondereza a Mboni za Yehova. M’bale Deschamp ananena kuti: “Mkulu wina wa boma yemwe anali Mkatolika ndipo ankagwira ntchito ku maofesi oona za katundu wolowa ndi wotuluka m’dziko, analanda mabuku athu ponena kuti anali onyoza chipani cha Nazi. Nditapita kukadandaula ku ofesiyi, munthu amene ndinam’peza anatibwezera mabuku athu nthawi yomweyo. Iye ananena kuti: ‘Abwana aja kulibe, tengani mabuku anuwa.’ Pa nthawiyi, mkulu wovutayo anali atapita kutchuthi ndipo amene anandithandizayo sanali Mkatolika.”

Mlongo Deschamp ananena kuti: “Nthawi ina, akuluakulu a boma anatiuza kuti tichotse zithunzi ziwiri zomwe zinali m’buku lotchedwa Enemies. Iwo anakwiya kwambiri ndi zithunzi  zosonyeza chinjoka chopiringizikapiringizika (Satana) komanso mkazi wachiwerewere yemwe anali ataledzera (chipembedzo chonyenga). Chinjokacho komanso mkazi wachiwerewereyo anajambulidwa atavala chipewa cha Papa. * Koma chifukwa choti tinkafunitsitsa kugawira bukuli, ine ndi anzanga ena awiri tinakhala pansi padoko lina, kukutentha kwambiri, n’kuyamba kufufuta zithunzizi m’mabuku onse omwe tinali nawo.”

Zithunzi ziwiri zomwe akuluakulu a boma analamula kuti zichotsedwe m’buku la Enemies

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kuyamba ku Europe, mabuku athu ananena mosapita m’mbali zinthu zachinyengo zimene atsogoleri a matchalitchi ankachita polowerera nkhani zandale. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri atsogoleriwo moti anakakamiza akuluakulu a boma kuti aletse ntchito yathu yolalikira ndipo mabuku athu angapo analetsedwa.

Komabe abale anapitiriza kulalikira ndipo anayamba kusindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina omwe analandira  kuchokera ku Australia. (Mac. 4:20) Pofotokoza zimene ankachita kuti akwanitse kugawira mabuku pa nthawiyi, mlongo Deschamp ananena kuti: “Tikasindikiza kabuku kapena magazini, tinkafunika kupita nawo kwa akuluakulu a boma kuti atipatse chilolezo tisanayambe kugawira mabukuwo. Komabe kumayambiriro kwa mlungu, tinkasindikiziratu mabukuwa n’kugawira abale kumipingo. Kumapeto kwa mlungu tinkatenga zimene tasindikizazo n’kupita nazo kwa mkulu wa oweruza milandu. Mkuluyo akanena kuti mabukuwo asagawidwe, tinkangonamizira kumva chisoni n’kubwerera kukapitiriza ntchito yathu.”

Abale ndi alongo amene ankagawira mabuku oletsedwa ankachita zinthu mochenjera kwambiri kuti asagwidwe ndi apolisi. Mwachitsanzo, M’bale Charles Harris akulalikira m’dera la Kediri ku East Java, mosadziwa anapita kunyumba ya mkulu wa apolisi wa m’deralo.

Wapolisiyo atangomuona ananena kuti: “Ndakhala ndikufunafuna anthu inu lero lonse. Ima pompo ndikatenge pamene ndinalembapo mabuku amene tinakuletsani.”

M’bale Harris ananena kuti: “Mkuluyo atalowa m’nyumba mwake, ndinabisa mabuku onse omwe analetsedwawo m’matumba a chijekete chomwe ndinavala. Atabwerera, ndinam’patsa timabuku 15 tomwe sitinali toletsedwa ndipo anapereka chopereka monyinyirika. Kenako ndinagawira mabuku oletsedwawo kwa anthu ena okhala m’deralo.”

Kusindikiza Mabuku pa Nthawi Yovuta

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayambika ku Europe, zinali zovuta kwambiri kuti abale athu ku Indonesia azilandira mabuku kuchokera m’dziko la Netherlands. Koma abale anali ataoneratu kuti padzakhala vutoli, choncho anakonza zoti mabuku azisindikizidwa ndi kampani ina mumzinda wa Jakarta. Magazini yoyamba kutuluka m’Chiindoneziya inali ya Consolation, yomwe panopa timati Galamukani! ndipo inali ya mwezi wa January 1939. Kenako anayambanso kusindikiza magazini ya Nsanja ya Olonda. Patapita nthawi, abale anagula makina aang’ono osindikizira mabuku ndipo anayamba kusindikiza okha mabukuwa. Mu 1940 abalewa analandira makina aakulu osindikizira mabuku  kuchokera ku Australia. Zitatero anayamba kusindikiza timabuku ndi magazini m’Chiindoneziya ndi m’Chidatchi ndipo ankagwiritsa ntchito ndalama zam’thumba mwawo.

Makina oyamba osindikizira mabuku akufika pamalo olandirira mabuku mumzinda wa Jakarta

Kenako pa 28 July, 1941, akuluakulu a boma analetsa mabuku onse ofalitsidwa ndi a Mboni. Mlongo Deschamp ananena kuti: “Tsiku lina ndikugwira ntchito mu ofesi, mwadzidzidzi kunatulukira apolisi atatu atavala yunifomu ndipo anali ndi mkulu wa apolisi wachidatchi. Sitinadabwe ndi zimenezi chifukwa masiku atatu izi zisanachitike, tinali titamva mphekesera zoti boma liletsa mabuku athu. Mkuluyo anawerenga chikalata chachitali chonena kuti boma laletsa mabuku athu. Kenako anatilamula kuti tipite naye ku ofesi komwe kunali makina osindikizira mabuku kuti akatsekeko. Koma mwamuna wanga anamuuza kuti anali atachedwa chifukwa makinawo anali atagulitsidwa dzulo lake.”

Koma akuluakulu a boma sanaletse Baibulo. Choncho abale anapitiriza kulalikira kunyumba ndi nyumba komanso kuphunzira ndi anthu pogwiritsa ntchito Baibulo lokha. Popeza nkhondo ya padziko lonse inali itafika poipa kwambiri ku Asia, apainiya onse anauzidwa kuti abwerere ku Australia.

^ ndime 1 Patapita nthawi, bambo ake a Felix ndi azing’ono awo anakhalanso a Mboni. Mchemwali wake Josephine, anakwatiwa ndi André Elias ndipo banjali linalowa Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Nkhani yonena za moyo wa Josephine Elias ili mu September 2009.

^ ndime 1 Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, m’baleyu anabwerera ku Australia ndipo patapita nthawi, anabereka ana. M’bale Rice anamaliza utumiki wake wa padzikoli m’chaka cha 1986.

^ ndime 3 Anajambula zithunzizi potengera zimene zili pa Chivumbulutso 12:9 ndi pa Chivumbulutso 17:3-6.