KUYAMBIRA pa 15 August mpaka pa 18 August, 1963, abale ndi alongo ambirimbiri a m’dziko la Indonesia, komanso abale 122 ochokera kumayiko ena anasonkhana mumzinda wa Bandung ku West Java. Anthuwa anabwera mumzindawu kuti adzachite msonkhano wamayiko wa mutu wakuti: “Uthenga Wabwino Wosatha.” Kameneka kanali koyamba kuti msonkhano wamayiko uchitike m’dziko la Indonesia.

Pa nthawi imene ankakonzekera msonkhanowu abale anakumana ndi mavuto ambiri. Abalewa anasintha malo ochitira msonkhanowu maulendo atatu chifukwa choti malo amene ankawapezawo, pankafunika kuchitikira zikondwerero za tsiku limene dzikoli linalandira ufulu wodzilamulira. Vuto lina linali loti chifukwa cha kuchepa mphamvu kwa ndalama ya m’dzikoli, mitengo yolipirira thiransipoti inakwera kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ena asinthe mayendedwe omwe anakonza poyamba. Mwachitsanzo, m’bale wina anayenda ulendo wapansi kwa masiku 6 kuti akapezeke pamsonkhanowu. Komanso chifukwa cha kuvuta kwa thiransipoti, anthu ena 70 ochokera ku Sulawesi anakwera pamwamba pa boti lomwe linali litadzaza kwambiri. Anthuwa anayenda ulendowu kwa masiku 5.

Abale ndi alongo a ku Indonesia anasangalala kwambiri kucheza ndi alendo a ku mayiko ena. Anasangalalanso kukumana ndi abale awiri a m’Bungwe Lolamulira omwe ndi M’bale Frederick Franz ndi M’bale Grant Suiter. M’bale wina amene anapezeka pamsonkhanowu ananena kuti: “Abale amene anabwera kumsonkhanowu ankachita kuonekeratu kuti akusangalala kwambiri.”

Anthu oposa 750 anapezeka pamsonkhanowu ndipo anthu 34 anabatizidwa. M’bale Ronald Jacka ananena kuti: “Msonkhanowu unathandiza anthu omwe ankaphunzira Baibulo kutsimikizira kuti apeza choonadi. Unalimbikitsanso abale a m’dzikoli kuti azigwira mwakhama ntchito yolalikira.”

M’bale Ronald Jacka (kumanja) akukamba nkhani pamsonkhano wamayiko wamutu wakuti, “Uthenga Wabwino Wosatha” ali ndi m’bale yemwe ankamasulira nkhani yake