Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Malonda a Zokometsera Chakudya

Malonda a Zokometsera Chakudya

M’ZAKA za m’ma 1500, malonda a zokometsera chakudya ndi amene ankabweretsa ndalama m’mayiko ambiri ngati mmene zilili ndi mafuta a galimoto masiku ano. Zilumba zomwe pa nthawiyo zinkadziwika kuti Spice Islands ndi zimene zinali zotchuka kwambiri pa nkhani yochita malondawa. Panopa zilumbazi zimadziwika ndi mayina akuti Maluku komanso North Maluku ndipo zili m’dziko la Indonesia. Anthu omwe ankachita malonda a zinthu zokometsera chakudya ankapeza ndalama zambiri akagulitsa zinthu monga nutmeg ndi cloves kumayiko a ku Europe.

Akatswiri ofufuza malo anatulukira njira zokafikira kuzilumba za Maluku ndi ku North Maluku. Akatswiriwa mayina awo anali Christopher Columbus, Vasco da Gama, Ferdinand Magellan, Samuel de Champlain komanso Henry Hudson. Zimene anachitazi zinathandiza kuti anthu amvetse bwino kwambiri mmene dziko lapansili lilili.