Pa 9 July, 1964, bungwe la Mboni za Yehova la Bible Students Association, linakalembetsa ku dipatimenti yoona zachilungamo m’dziko la Indonesia kuti likhale bungwe lovomerezeka mwalamulo. Koma kuti abale azisonkhana komanso kulalikira mwaufulu, anayenera kukalembetsanso ku nthambi yoona za ufulu wa zipembedzo. A ku dipatimentiyi ankafunika kuyankhulana kaye ndi a ku nthambi yoona za chikhalidwe cha anthu a m’zipembedzo zachikhristu. Koma akuluakulu ambiri a ku nthambiyi anali achipembedzo chachipulotesitanti omwe ankadana ndi a Mboni za Yehova.

Tsiku lina m’bale wina anakumana ndi munthu yemwe ankagwira ntchito ndi nduna yoona za ufulu wa zipembedzo. Anthuwa anazindikira kuti ankachokera mudzi umodzi, choncho anacheza kwambiri m’chinenero chawo. M’baleyo anafotokozera munthuyo mavuto omwe a Mboni za Yehova ankakumana nawo akapita ku nthambi yoona za zipembedzo zachikhristu. Ndiyeno munthuyo anakonza zoti abale atatu akakumane ndi nduna yoona za ufulu wa zipembedzo.  Ndunayi inali Msilamu ndipo anali munthu wachifundo komanso wokoma mtima. Choncho pa 11 May, 1968, ndunayi inapereka chikalata chonena kuti a Mboni za Yehova ndi chipembedzo chovomerezeka ndipo ali ndi ufulu wosonkhana komanso kugwira ntchito yolalikira.

Ndunayi inadziperekanso kuthandiza a Mboni za Yehova ochokera m’mayiko ena kupeza ziphaso zolowera m’dzikolo mosachita kupempha chilolezo kuchokera ku nthambi yoona za zipembedzo zachikhristu. Inathandizanso kuti amishonale 64 aloledwe kukhala m’dziko la Indonesia.

Pofika m’chaka cha 1968, amishonale pafupifupi 300 ndi apainiya apadera komanso ofalitsa oposa 1,200, ankalalikira uthenga wabwino m’dziko lonse la Indonesia. Amishonale anaphunzitsa abale ambiri a m’dzikoli ndipo zimenezi zinathandiza kuti akhale okhwima mwauzimu. Zimene abalewa anaphunzira zinawathandiza pa nthawi imene anakumana ndi mavuto.

Atsogoleri a Zipembedzo Anapatsidwa “Mphatso ya Khirisimasi”

M’chaka cha 1974, nthambi yoona za zipembedzo zachikhristu inayambiranso kufunafuna njira yoti ntchito ya Mboni za Yehova iletsedwe. Mkulu wa nthambi yoona za zipembedzo zachikhristuyu analemba kalata yopita m’zigawo zonse komwe kunali maofesi a nthambi yoona za ufulu wa zipembedzo. M’kalatayo analembamo kuti a Mboni za Yehova ndi gulu losavomerezeka ndi boma. Iye analimbikitsa akuluakuluwo kuti akaona kuti a Mboni akuwavutitsa asamawathandize. Imeneyitu inali njira yowauzira kuti azizunza a Mboni za Yehova. Anthu ambiri ogwira ntchito ku maofesiwa sankatsatira malangizo amenewa. Komabe anapezerapo mwayi woletsa a Mboni kuti asamachite misonkhano yawo komanso kulalikira kunyumba ndi nyumba.

Pa 24 December, 1976, nyuzipepala ina inalengeza kuti ntchito ya Mboni za Yehova yaletsedwa

Pa nthawiyi, bungwe loona za zipembedzo padziko lonse, linakonza zochita msonkhano wa mayiko ku Jakarta koma Asilamu sanagwirizane ndi zimenezi. Kenako bungweli linalengeza  kuti silichititsa msonkhano wake chifukwa chakuti zipembedzo zinkalimbana. Nkhani yomwe inkadetsa nkhawa atsogoleri a ndale inali yoti Akhristu asamakope anthu a zipembedzo zina kuti alowe Chikhristu. Choncho atsogoleri achipembedzo anapezerapo mwayi woimba mlandu a Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo yolalikira. Zomwe atsogoleriwa ankanenazi zinachititsa kuti akuluakulu a boma ambiri ayambe kudana ndi a Mboni za Yehova.

Pofika mu December 1975, pamene mavuto a zachipembedzo anapitiriza kuwonjezereka, dziko la Indonesia linayamba kumenyana ndi dziko la Timor-Leste (lomwe kale linali East Timor). Pa nthawiyi, dzikoli linkalamulidwa ndi dziko la Portugal. Patapita miyezi 7, dziko la Timor-Leste linayamba kulamuliridwa ndi dziko la Indonesia ndipo anthu a m’dzikoli anayamba kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Koma abale sanalowerere ndale, kulowa ntchito ya usilikali kapena kuchitira sailuti mbendera. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri akuluakulu a asilikali. (Mat. 4:10; Yoh. 18:36) Pofuna kuthana ndi a Mboni za Yehova, atsogoleri achipembedzo analimbikitsa boma kuti liletse ntchito yawo. Kenako chapakatikati pa mwezi wa December 1976, boma la dzikoli linalengeza kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chaletsedwa. Ndiye popeza zimenezi zinachitika m’mwezi wa December, zinali ngati atsogoleri achipembedzo aja apatsidwa “mphatso ya khirisimasi” moti anasangalala kwambiri.