M’bale Alexander MacGillivray, yemwe anali mtumiki wa nthambi ku Australia, anali mu ofesi yake ndipo ankaganizira za nkhani inayake yofunika kwambiri. Nkhaniyi anali ataigainizira kwa masiku angapo ndipo inali yokhudza zilumba za m’dziko la Indonesia kumene kunalibe aliyense wolalikira. Kenako anaganiza zoti acheze ndi M’bale Frank Rice.

M’bale Rice, anali ndi zaka 28 ndipo anali atangofika kumene pa ofesi ya nthambi ya ku Australia. Iye anaphunzira choonadi ali wachinyamata, kenako anayamba kutumikira monga kopotala kapena kuti mpainiya. Pamene ankachita upainiyawo anapirira mavuto ambiri. Anali wakhama kwambiri moti kwa zaka zoposa 10 analalikira m’madera ambiri m’dziko la Australia. Iye ankayenda pa hatchi, pa njinga yakapalasa, pa njinga yamoto komanso pa galimoto yokhala ndi kalavani yomwe ankagonamo. Atakhala ku Beteli kwa nthawi yochepa, M’bale Rice anali wokonzeka kukayamba utumiki wake kugawo latsopano.

M’bale MacGillivray anaitana M’bale Rice mu ofesi yake. Kenako anatenga mapu n’kumulozera zilumba zomwe zinali kumpoto kwa dziko la Australia. Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi ungakonde kukayamba kulalikira kudera ili? Kulibe m’bale aliyense kuzilumba zimenezi.”

M’bale Rice anakopeka ndi zilumba zambirimbiri zomwe zinkaoneka ngati miyala ya mtengo wapatali m’nyanja ya India. Zilumba zake zinali za Netherlands East Indies zomwe panopa ndi dziko la Indonesia. * Iye anavomera kukalalikira m’derali ndipo analoza likulu la dzikoli (lomwe panopa ndi Jakarta) n’kunena kuti: “Ndikufuna kukayambira apa.” Pazilumbazi pankakhala  anthu ambirimbiri omwe anali asanamvepo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

Kulalikira Pachilumba cha Java

Mu 1931, M’bale Rice anafika mumzinda wa Jakarta womwe ndi waukulu komanso wodzaza ndi anthu pachilumba cha Java. Iye anachita lendi nyumba ina pafupi ndi mzindawu ndipo ankasungamo makatoni ambirimbiri a mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Mwiniwake wa nyumbayo anali mzimayi ndipo anadabwa kwambiri ndi kuchuluka kwa mabukuwo.

M’bale Frank Rice ndi M’bale Clem Deschamp ku Jakarta

M’bale Rice anati: “Poyamba ndinkasowa wocheza naye ndipo zimenezi zinkachititsa kuti ndizingoganizira zakunyumba. Ndinkangoona anthu atavala zovala zomwe anthu amavala nthawi yotentha. Koma ineyo ndinali ndidakali ndi zovala zanga zokhuthala  zogwirizana ndi nyengo ya ku Australia moti ndinkamva kutentha kwambiri. Komanso sindinkadziwa Chidatchi kapena Chiindoneziya. Ndiyeno ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Kenako ndinaganiza zopita kumalo kumene anthu amagulitsa malonda kuti ndikakumane ndi anthu oyankhula Chingelezi. Kumeneku n’kumene ndinayambira kulalikira ndipo zinthu zinayenda bwino kwambiri.”

Popeza kuti anthu ambiri ku Jakarta ankalankhula Chidatchi, M’bale Rice anachita khama kwambiri kuphunzira chiyankhulochi moti pasanapite nthawi yaitali anayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Anayambanso kuphunzira Chiindoneziya ndipo anachidziwa. M’bale Rice anati: “Koma vuto linali loti ndinalibe magazini alionse a m’Chiindoneziya. Ndiyeno tsiku lina, Yehova anandichititsa kukumana ndi mphunzitsi wina woyankhula Chiindoneziya yemwe anachita chidwi ndi choonadi. Nditamupempha kuti amasulire kabuku kakuti, Kodi Akufa Ali Kuti?, analola. Pasanapite nthawi anamasuliranso mabuku ena ndipo anthu ambiri oyankhula Chiindoneziya anayamba kuphunzira Baibulo.”

Mu November 1931, apainiya ena awiri ochokera ku Australia anafikanso ku Jakarta. Mayina awo anali Clem Deschamp wa zaka 25 ndi Bill Hunter wa zaka 19. M’bale Clem ndi Bill ankayenda ndi kalavani yokokedwa ndi galimoto yomwe ankagonamo. Kalavaniyo inali imodzi mwa makalavani oyambirira kufika ku Indonesia. Anyamatawa ataphunzira mawu ochepa a Chidatchi, anayamba kulalikira m’mizinda ikuluikulu ya ku Java.

M’bale Charles Harris akuyenda panjinga komanso akugwiritsa ntchito kalavani polalikira

Mpainiya winanso amene anabwera pambuyo pa abalewa anali Charles Harris. M’baleyu anali munthu wolimba mtima ndipo kwawo kunali ku Australia. Kuyambira mu 1935, m’baleyu analalikira m’madera ambiri a ku Java. Ankayenda ndi kalavani yomwe inkakokedwa ndi galimoto ndipo nthawi zina akamakalalikira, ankayenda pa njinga yake. M’baleyu ankagawira mabuku a m’zinenero zokwana 5. Zinenero zake zinali Chiarabu, Chitchainizi, Chidatchi, Chingelezi komanso Chiindoneziya. Nthawi zina m’baleyu ankagawira mabuku ochuluka kwambiri moti kwa zaka zingapo anagawirapo mabuku pafupifupi 17,000.

 Chifukwa cha kuchuluka kwa mabuku amene M’bale Harris anagawira, anthu ambiri anachita chidwi ndipo ankafuna kudziwa zambiri. Mwachitsanzo, mkulu wina waboma ku Jakarta, anafunsa M’bale Deschamp kuti: “Kodi ku East Java kuli anthu angati amene akugwira ntchito yanuyi?”

M’bale Deschamp anayankha kuti: “Kuli munthu mmodzi basi.”

Mkuluyo anatsutsa mwamphamvu kuti: “Ayi, sindingakhulupirire zimenezo. Mabuku amene mwagawirawa akusonyeza kuti pali anthu ambiri amene akugwira ntchitoyi.”

Apainiya omwe anali oyamba kufika m’dzikoli ankasamukasamuka n’cholinga choti athandize anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. M’bale Hunter ananena kuti: “Tikafika pachilumba tinkalalikira pachilumba chonsecho ndipo nthawi zambiri  sitinkayankhula ndi munthu maulendo awiri.” Pa nthawi imene apainiyawa ankasamukasamuka, ankafesa mbewu za choonadi zomwe patapita nthawi zinabala zipatso.—Mlal. 11:6; 1 Akor. 3:6.

Anthu a Pachilumba cha Sumatra Anamva Uthenga Wabwino

Chaka cha 1936 chitayandikira, apainiya a ku Java anakambirana zimene angachite kuti akalalikire ku Sumatra. Chilumbachi ndi cha nambala 6 pa zilumba zikuluzikulu padziko lonse. Pachilumbachi pali mizinda ikuluikulu ndipo chili pakatikati pa dziko lapansi komanso kuli mapiri ndi nkhalango zambiri zowirira.

Apainiyawa anagwirizana zoti atumizeko M’bale Rice ndipo anasonkherana ndalama zoti m’baleyu akagwiritse ntchito. Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Rice anafika mumzinda wa Medan ku North Sumatra atanyamula zikwama ziwiri zoti azigwiritsa ntchito polalikira. Ananyamulanso makatoni 40 a mabuku ndipo anali ndi ndalama zochepa. Chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba, m’baleyu anayamba kulalikira atangofika. Ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza pogwira ntchito yolalikirayi.—Mat. 6:33.

Mlungu womaliza umene M’bale Rice analalikira mumzinda wa Medan, anakumana ndi munthu wina wachidatchi yemwe anamupempha kuti akamwe naye limodzi khofi. M’baleyu anauza munthuyo kuti akufuna galimoto kuti akwanitse kulalikira uthenga wabwino pachilumba chonsecho. Munthuyo analoza galimoto yomwe inali yowonongeka n’kuuza m’baleyu kuti: “Ngati ungakwanitse kukonza galimotoyi, ukhoza kuigula pamtengo wa magiuda 100.” *

M’bale Rice anayankha kuti: “Sindikwanitse kupeza ndalama zimenezo.”

Kenako munthuyo anayang’ana m’baleyo n’kumufunsa kuti: “Kodi ukufunadi kulalikira pachilumba chonse cha Sumatra?”

Poyankha M’bale Rice anati: “Inde.”

Pamenepo bambo uja ananena kuti: “Chabwino. Ukhoza kutenga galimotoyi ngati ungakwanitse kuikonza. Ukadzapeza ndalamazo udzandipatse.”

 M’bale Rice anayamba kukonza galimotoyo ndipo pasanapite nthawi inayamba kuyenda bwinobwino. Kenako M’bale Rice analemba kuti: “Ndinanyamuka ulendo wokalalikira anthu a ku Sumatra nditadzadza mabuku m’galimoto, ndili ndi mafuta okwanira komanso ndili ndi chikhulupiriro champhamvu kuti zinthu zikandiyendera bwino.”

M’bale Henry Cockman ali ndi M’bale Clem ndi Mlongo Jean Deschamp ku Sumatra, mu 1940

Pamene chaka chimodzi chinkatha, n’kuti M’bale Rice atamaliza kulalikira pachilumba chonsecho ndipo kenako anabwerera ku Jakarta. Atafika ku Jakarta anagulitsa galimoto ija ndalama zokwana magiuda 100, n’kuzitumiza kwa munthu wachidatchi uja ku Medan.

Patadutsa milungu ingapo, M’bale Rice analandira kalata kuchokera ku ofesi ya nthambi ya ku Australia yomuuza kuti apite kukachita upainiya kudera lina. Nthawi yomweyo analongedza katundu wake n’kuyamba ulendo wokachita utumiki wake watsopano ku Indochina, komwe panopa ndi dziko la Cambodia, Laos ndi Vietnam.

^ ndime 4 Poyamba dzikoli linkadziwikanso kuti Dutch East Indies. Pa nthawi imene abalewa ankakambirana nkhaniyi, Adatchi anali atalamulira dzikoli kwa zaka 300. Adatchiwa ankachita bizinezi yogula ndi kugulitsa zokometsera zakudya. M’nkhaniyi tigwiritsa ntchito mayina a malo omwe anthu akuwadziwa panopa.

^ ndime 3 Ndalamazi ndi zofanana ndi madola pafupifupi 1,100 a ku America.