Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Akulalikira mumsika wina ku Jakarta

 INDONESIA

Ntchito Yathu Inayambanso Kuyenda Bwino

Ntchito Yathu Inayambanso Kuyenda Bwino

Atsogoleri amatchalitchi amene amati ndi achikhristu atamva kuti a Mboni za Yehova apatsidwa ufulu woti azigwira ntchito yawo, anakwiya koopsa. Atsogoleri achipembedzo oposa 700 pamodzi ndi anthu ena a maudindo m’matchalitchi awo, anachita msonkhano ku Jakarta pofuna kukakamiza boma kuti lipitirize kuletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Koma boma silinalole zimenezi.

Anthu ena a maganizo abwino atamva kuti a Mboni si oletsedwanso m’dzikoli, analemba makalata opita ku ofesi ya nthambi opempha kuti awatumizire mabuku komanso anthu oti aziwaphunzitsa Baibulo. M’chaka cha 2003, anthu oposa 42,000 anapezeka pamwambo wa Chikumbutso ndipo chiwerengerochi chinali kuwirikiza kawiri chiwerengero cha ofalitsa m’dzikoli. Anthu pafupifupi 10,000 anapezeka pamsonkhano waukulu ku Jakarta ndipo munthu wina yemwe anali ndi udindo waukulu ku nthambi yoona za ufulu wachipembedzo anabwera pamsonkhanowu. Mkuluyu anadabwa kwambiri kuona achinyamata komanso achikulire akumvetsera nkhani komanso akuwerenga Malemba amene okamba nkhani ankawatchula. Munthuyu ananena kuti ayesetsa kuthandiza anthu kudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi anthu abwino kwambiri.

Ntchito ya Mboni itatsegulidwa m’dzikoli, amishonale omwe anapita kwawo aja anayambanso kubwerera ku Indonesia. Ena mwa amishonalewa anali Josef ndi Herawati Neuhardt * (a ku Solomon Islands), Esa ndi Wilhelmina Tarhonen (a ku Taiwan), Rainer ndi Felomena Teichmann (a ku Taiwan), komanso Bill ndi Nena Perrie (a ku Japan). Kenako kunafikanso amishonale ena omwe anali atangomaliza kumene maphunziro a Sukulu ya Giliyadi. Amishonale atsopanowa anatumizidwa ku North  Sumatra, ku Kalimantan, ku North Sulawesi ndi kumadera ena akutali.

‘Ndinkasangalala kwambiri kuthandiza ophunzira kuti aziphunzitsa mwaluso komanso kuti azikamba nkhani mogwira mtima.’—Julianus Benig

M’chaka cha 2005, ofesi ya nthambi inachititsa makalasi awiri ophunzitsa Baibulo. M’bale Julianus Benig ndi mmodzi mwa alangizi a Sukulu Yophunzitsa Utumiki, yomwe masiku ano imadziwika kuti Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Iye ananena kuti: “Ndinkasangalala kwambiri kuthandiza ophunzira kuti aziphunzitsa mwaluso, azikamba nkhani mogwira mtima komanso kuti azichita zinthu zothandiza gulu la Mulungu.” Ambiri amene anamaliza sukuluyi, tsopano ndi apainiya apadera kapena oyang’anira madera. Abale ambiri amene analowa m’kalasi yoyamba ya sukulu ya oyang’anira oyendayenda * anali ataphunzira ntchito yawoyo pa nthawi imene ntchito ya Mboni inali yoletsedwa. Choncho sukuluyi inathandiza abalewa kuti azikwanitsa kuchita utumiki wawo mogwira mtima, ntchito yathu itavomerezedwanso. M’bale Ponco Pracoyo amene analowa  m’kalasi yoyamba ananena kuti: “Sukuluyi inandithandiza kwambiri kuti ndizimvera anthu ena chifundo komanso kuti ndizidzipereka ndi mtima wonse pamene ndikutumikira monga woyang’anira dera. Kunena zoona sukuluyi inandithandiza kwambiri.”

Pankafunika Nyumba za Ufumu

Pa zaka 25 zimene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Indonesia, misonkhano inkachitikira m’nyumba za abale. Mipingo yochepa ndi imene inakwanitsa kumanga Nyumba za Ufumu ndipo zinali zovuta kupeza chilolezo chomangira nyumbazi. Chifukwa choti m’mipingo yambiri munali ofalitsa ochuluka, ofesi ya nthambi inakonza zoti pakhale Dipatimenti Yoyang’anira Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu kuti izithandiza pa ntchitoyi. Panopa dipatimentiyi imadziwika kuti Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga.

Mipingo yoyambirira kuthandizidwa pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumuyi inali ya pachilumba cha Nias ku North Sumatra. M’bale Haogo’aro Gea yemwe wakhala kwa nthawi yaitali mumpingo wa Gunungsitoli anati: “Titamva kuti atimangira Nyumba ya Ufumu, tinasangalala kwabasi. Ofesi ya nthambi inatumiza abale 7 kuti adzayang’anire ntchitoyi. Tinamaliza kumanga Nyumba ya Ufumuyi mu 2001.” M’bale Faonasökhi Laoli wa mu komiti yomanga ya m’deralo, anati: “Poyamba tinkasonkhana m’nyumba za abale moti anthu ena ankatinyoza chifukwa cha zimenezi. Koma atatimangira Nyumba ya Ufumu, chiwerengero cha anthu obwera kumisonkhano chinakwera kuchoka pa 20 kufika pa 40. Pamene chaka chinkatha, chiwerengero cha anthu osonkhana chinawirikiza ka 5. M’dera lathu lonse palibe nyumba yopempherera yokongola kuposa nyumba yathu ya ufumuyi ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu azitilemekeza.”

Nyumba ya Ufumu ya ku Bandung

Mu 2006 abale a mumzinda wa Bandung ku West Java anayamba kufufuza malo omangapo Nyumba ya Ufumu yomwe inali yoyamba mumzindawo. M’bale Singap Panjaitan amene ankatumikira mu komiti yomanga ananena kuti: “Zinatitengera miyezi 12 kuti tipeze malo abwino omangapo nyumbayi.  Tinkafunikanso kupempha chilolezo kwa anthu 60, omwe ankakhala m’dera limene tinkafuna kumanga Nyumba ya Ufumuyo, tisanapite kuboma kuti akatipatse chikalata chotivomereza kumanga nyumbayo. Anthu 76 anavomereza zoti tikhoza kumanga m’derali kuphatizapo mayi wina wotchuka yemwe poyamba ankatitsutsa. Nyumba ya Ufumuyo itatha, tinaitana anthu a m’deralo komanso meya wa ku Bandung kuti adzaione. Meyayo anati: ‘Anthu amatchalitchi ena akamamanga matchalitchi awo azitengera nyumba yokongolayi.’” Nyumba ya Ufumuyi ndi yosanjikiza ndipo anaipatulira mu 2010.

Kuyambira mu 2001, Nyumba za Ufumu zoposa 100 zamangidwa ku Indonesia. Komabe padakali mipingo yambiri imene ikufunika Nyumba za Ufumu.

^ ndime 3 Nkhani yofotokoza mbiri ya Mlongo Herawati Neuhardt inatuluka mu Galamukani! ya February 2011.

^ ndime 1 Panopa sukuluyi imadziwika kuti Sukulu ya Oyang’anira Madera ndi Akazi Awo.