Nthawi imene ntchito ya Mboni inaletsedwa ku Indonesia, abale ndi alongo ambiri anapitirizabe kusonkhana m’nyumba za abale. Kuti anthu asawazindikire, sankaimba nyimbo pa nthawi ya misonkhano. Nthawi zina apolisi ankafika pamisonkhanoyi koma abale ankachita zinthu modekha.

Nthawi zina abale ankagwiritsa ntchito nthawi imene mabanja angapo akumana kapena nthawi ya mwambo waukwati kuti achite misonkhano ikuluikulu. M’bale Tagor Hutasoit ananena kuti: “Amene akukwatirana ankalembetsa ukwati wawo ku boma ndipo kenako ankapempha chilolezo ku polisi kuti akhale ndi mwambo wa ukwati pomwe padzakhale anthu ambiri. Ikafika nthawi ya phwando la ukwati, akwati ndi anthu ogwirizira ankakhala papulatifomu ndipo abale ankakamba nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo.”

Nthawi ina abale ali pamsonkhano, wapolisi anafika ndipo anakumana ndi M’bale Hutasoit.

Wapolisiyo anafunsa m’baleyu kuti: “Maukwati ambiri amatenga maola awiri kapena atatu basi. N’chifukwa chiyani maukwati anu amatenga tsiku lonse lathunthu?”

M’bale Hutasoit anayankha kuti: “Ena amene akumangitsa ukwati amakhala ndi mavuto ambiri moti amafunikira kuwapatsa malangizo ambiri a m’Baibulo amene angawathandize.”

Wapolisiyo anangogwedeza mutu n’kunena kuti: “Ayi, koma n’zomveka.”

 M’chaka cha 1983, abale anakamba nkhani zina za pamsonkhano wachigawo wa mutu wakuti, “Mgwirizano wa Ufumu” pamwambo wa maukwati angapo amene anachitikira pasitediyamu ina yaikulu ku Jakarta. Abale pamodzi ndi anthu ena amene ankaphunzira nawo Baibulo pafupifupi 4,000 anapezeka pamsonkhanowu ndipo anthu 125 anabatizidwa pamalo ena, msonkhanowu usanayambe. Patapita nthawi, apolisi anasiya kulondalonda kwambiri abalewa ndipo zimenezi zinachititsa kuti achite msonkhano waukulu umene panapezeka anthu pafupifupi 15,000.

 Anamanga Ofesi ya Nthambi pa Nthawi Imene Ntchito Yathu Inali Yoletsedwa

M’zaka za m’ma 1980 ndi 1990, ofesi ya nthambi inalemba makalata opita ku boma mobwerezabwereza kuti lilolenso ntchito ya a Mboni za Yehova ku Indonesia. Abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana analembanso makalata opita ku boma la dzikoli komanso kwa akazembe, pofuna kudziwa chifukwa chake a Mboni za Yehova analetsedwa m’dzikoli. Akuluakulu ambiri a boma anagwirizana ndi zoti a Mboni za Yehova aloledwe kuti azigwira ntchito yawo mwaufulu. Koma mkulu wa ku ofesi ina, ku nthambi yoona za chikhalidwe cha anthu m’zipembedzo zachikhristu, ndi amene ankalepheretsa zimenezi.

Mu 1990, abale anaona kuti zinali zotheka kumanga ofesi ya nthambi kudera lina kumene anthu sakanawazindikira. M’chaka chomwechi, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale agule malo pafupi ndi mzinda wa Bogor, womwe ndi mzinda waung’ono ndipo uli pamtunda wa makilomita 40 kum’mwera kwa mzinda wa Jakarta. Komabe m’derali munali abale ochepa omwe anali ndi luso la zomangamanga. Ndiye kodi zikanatheka bwanji kuti amange maofesiwa?

Abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana anabwera kuti adzathandize kugwira nawo ntchitoyi. A ku Ofesi Yoyang’anira Ntchito ya Zomangamanga ku Brooklyn komanso Ofesi ya Chigawo Yoyang’anira Ntchito Zomanga ku Australia ndi amene anapereka mapulani omangira nyumbayi. Anthu pafupifupi 100 ochokera m’mayiko osiyanasiyana anabwera m’dzikoli kuti adzathandize kugwira nawo ntchitoyi, yomwe inatenga zaka ziwiri.

M’bale Hosea Mansur amene ankaimira abale poyankhula ndi akuluakulu a boma ananena kuti: “Akuluakulu a boma omwe anali Achisilamu anaona zilembo zoyambirira za dzina langa pachipewa chomwe ndinkavala pogwira ntchitoyi, zomwe ndi H.M. Iwo ataona zimenezi anayamba kuganiza kuti H akuimira Hājjī, lomwe ndi dzina limene anthu amene anapitako ku Mecca amapatsidwa powalemekeza. Zimenezi zinawachititsa  kuti azindilemekeza kwambiri komanso zinathandiza kuti ntchito yathu iyende bwino.”

Ofesi ya nthambi inamangidwa pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa

Mwambo wotsegulira ofesi ya nthambiyi unachitika pa 19 July, 1996. M’bale John Barr, yemwe anali m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani yopatulira ofesiyi. Pamwambowu panapezeka anthu 285. Anthu 118 anali oimira nthambi zina komanso ena anali anthu omwe anatumikirapo ngati amishonale. Panalinso anthu 59 omwe ankatumikira pabeteli ya m’dzikoli. Patapita masiku awiri, anthu 8,793 anapezeka pamsonkhano wachigawo wa mutu wakuti, “Amithenga a Mtendere Waumulungu” mumzinda wa Jakarta.

Yehova Amapulumutsa Anthu Ake

M’chaka cha 1998, Pulezidenti Soeharto (kapena kuti Suharto), yemwe analamulira dziko la Indonesia kwa nthawi  yaitali, anatula pansi udindo wake. Izi zitachitika, abale anayesetsa kuchita chilichonse chotheka kuti ntchito yathu ikhale yovomerezeka.

M’chaka cha 2001, mlembi wamkulu wa dziko la Indonesia, a Djohan Effendi, anapita ku New York kukacheza. Ali kumeneko anapita kukaona likulu lathu ku Brooklyn ndipo anakumana ndi abale atatu a m’Bungwe Lolamulira. Iwo anasangalala kwambiri ndi zimene anaona ndipo ananena kuti a Mboni za Yehova ali ndi mbiri yabwino padziko lonse lapansi. Kenako a Effendi anagwirizana ndi zoti a Mboni aloledwe kumagwira ntchito yawo mwaufulu ku Indonesia. Ananenanso kuti a Marzuki Darusman, omwe anali mkulu wa oweruza milandu, ndi amene anali ndi mphamvu zovomereza a Mboni kugwira ntchito yawo mwaufulu.

Nayenso mkulu wa oweruza milandu uja anagwirizana ndi zoti a Mboni azigwira ntchito yawo mwaufulu. Koma anthu ena amene ankagwira nawo ntchito sankagwirizana ndi zimenezi. Choncho anthuwa ankalepheretsa kuti a Mboni apatsidwe ufulu ndipo anali ndi maganizo oti munthu wina adzalowa m’malo mwa mkulu wa oweruza milandu uja. Kenako pa 1 June, 2001, M’bale Tagor Hutasoit anaitanidwa kuti akaonekere kwa mkulu wa oweruza milandu uja. M’baleyu anati: “Zaka 25 m’mbuyomo, ndinaitanidwanso mu ofesi yomweyo ndipo anandipatsa chikalata chonena kuti ntchito ya Mboni za Yehova yaletsedwa m’dziko la Indonesia. Koma pa tsikuli, lomwe linalinso tsiku lomaliza la mkuluyo kugwira ntchito, anandipatsa chikalata choperekanso ufulu kwa Mboni za Yehova.”

Pa 22 March , 2002, a Mboni za Yehova a m’dziko la Indonesia analembetsa ku nthambi yoona za ufulu wa chipembedzo ndipo boma linawavomereza kuti azigwira ntchito yawo mwaufulu. Mkulu wa nthambiyi anauza abale omwe ankaimira ofesi ya nthambi kuti: “Sichikalatachi chimene chikukupatsani ufulu wopembedza. Mulungu ndi amene wakupatsani ufulu umenewu. Chikalatachi chikungosonyeza kuti mwalembetsa ku boma kuti mukhale ovomerezeka. Panopa muli ndi ufulu ngati zipembedzo zina zonse ndipo boma ndi lokonzeka kukuthandizani.”