Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

 INDONESIA

Ankaona Kuti Kukhala pa Ubwenzi ndi Yehova N’kofunika Kwambiri

Thio Seng Bie

Ankaona Kuti Kukhala pa Ubwenzi ndi Yehova N’kofunika Kwambiri
  • CHAKA CHOBADWA 1906

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1937

  • MBIRI YAKE Anthu anamuchitira zinthu zankhanza chifukwa cha tsankho koma anapirira komanso anatumikira mokhulupirika monga mkulu mumpingo.—Yofotokozedwa ndi mwana wake wamkazi dzina lake Thio Sioe Nio.

M’MWEZI wa May, m’chaka cha 1963, anthu a ku West Java anayamba kuchita zipolowe polimbana ndi anthu ochokera m’dziko la China. Pa nthawiyi tinkakhala mumzinda wa Sukabumi, kumene bambo anga ankachita bizinezi yonyamula katundu pamagalimoto akuluakulu. Mumzindawu munkachitika kwambiri zipolowe poyerekeza ndi mizinda ina. Mwachitsanzo, tsiku lina anthu olusa kuphatikizapo anthu amene tinayandikana nawo nyumba anathyola chitseko n’kulowa m’nyumba yathu. Tinachita mantha kwambiri n’kukabisala ndipo anthuwo anaba katundu wathu.

Gulu la anthu olusawa litapita, anthu ena okoma mtima omwe tinayandikana nawo nyumba anabwera kudzatilimbikitsa. Pamene bambo anga ankacheza ndi anthuwo, anapeza Baibulo la Chisunda pa zinthu zimene anthu achipolowe aja anasiya. Kenako anatsegula Baibulolo n’kufotokozera anthu amene anabwera kudzatilimbikitsawo kuti Baibulo linali litaneneratu kuti zinthu ngati zimenezi zidzachitika. Anafotokozanso zimene Ufumu wa Mulungu udzachite m’tsogolo.

Bambo anga sankaganizira kwambiri za chuma cha padzikoli chifukwa nthawi zambiri ankatiuza kuti: “Muziika patsogolo zinthu zauzimu.” Chifukwa choti bambo anga ankaona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri, zinathandiza kuti mayi anga, azichimwene ndi azichemwali anga, agogo anga azaka 90, achibale athu ambirimbiri komanso anthu oyandikana nafe nyumba aphunzire choonadi n’kukhala a Mboni za Yehova.