Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Mpingo wa Surabaya mu 1954

 INDONESIA

Amishonale Anayamba Kufika ku Indonesia

Amishonale Anayamba Kufika ku Indonesia

M’mwezi wa July, 1951, mpingo wa ku Jakarta womwe unali ndi ofalitsa ochepa unasonkhana kuti ulandire M’bale Peter Vanderhaegen. M’baleyu anali mmishonale woyamba kufika m’dziko la Indonesia ndipo anali atangomaliza kumene maphunziro a Sukulu ya Giliyadi. Pamene chaka cha 1951 chinkatha, m’dzikoli munali mutafika amishonale ena 13 kuchokera ku Australia, Germany ndi ku Netherlands. Kubwera kwa amishonalewa kunachititsa kuti chiwerengero cha ofalitsa chiwonjezeke kwambiri.

Mlongo Fredrika Renskers, yemwe ndi mmishonale wachidatchi, ananena kuti: “Ndisanapite ku Indonesia ndinkaganiza kuti ndizikagwiritsa ntchito manja poyankhula ndi anthu komanso polalikira kunyumba ndi nyumba. Koma ndinasangalala kuona kuti anthu ambiri ankayankhula Chidatchi moti masiku oyamba ndinkalalikira m’chinenerochi.” M’bale Ronald Jacka, yemwe anachokera ku Australia, anati: “Enafe tinkagwiritsa ntchito kakhadi kolalikirira komwe kanali ndi mawu a Chiindoneziya. Ndikafika pakhomo la munthu ndinkawerenganso mawu a pakakhadiko kuti ndiwaloweze, kenako ndinkagogoda.”

Popeza amishonale ankathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira, chiwerengero cha ofalitsa chinawonjezeka mofulumira kuchoka pa ofalitsa 34 kufika pa ofalitsa 91 m’chaka chimodzi chokha. Kenako pa 1 September, 1951, ofesi ya nthambi inakhazikitsidwa kunyumba ya M’bale André Elias, yemwe ankakhala ku Central Jakarta. M’bale Ronald Jacka ndi yemwe anali mtumiki wa nthambi.

Anayamba Kulalikira M’madera Enanso

Mu November 1951, M’bale Vanderhaegen anatumizidwa ku North Sulawesi mumzinda wa Manado, komwe kunali M’bale Theo Ratu ndi mkazi wake. M’bale Ratu anali atakhazikitsa kagulu komwe kankasonkhana mumzindawu. Anthu ambiri m’derali anali a matchalitchi ena ndipo ankakonda Mawu a Mulungu. Choncho abalewa akamalalikira, anthuwo ankawalandira ndi manja awiri moti ankawalowetsa m’nyumba zawo. Kenako ankawapempha kuti awafotokozere mfundo za m’Baibulo. Nthawi zambiri  m’nyumbamo munkakhala anthu 10. Koma pakapita nthawi yochepa, anthuwo ankachuluka n’kufika pa 50. Pakamatha ola limodzi, pankakhala patafika anthu 200 moti ankatuluka m’nyumbamo n’kukakhala panja.

Chakumayambiriro kwa chaka cha 1952, M’bale Albert ndi Mlongo Jean Maltby anakhazikitsa nyumba ya amishonale mumzinda wa Surabaya, ku East Java. Mzinda wa Surabaya ndi mzinda wachiwiri pa mizinda ikuluikulu ya ku Indonesia. Kenako kunabweranso alongo ena 6 omwe anali amishonale ndipo mayina awo anali Gertrud Ott, Fredrika Renskers, Susie ndi Marian Stoove, Eveline Platte komanso Mimi Harp. Mlongo Fredrika ananena kuti: “Anthu ambiri a m’tauniyi anali Asilamu ndipo anali ochezeka. Zinkaoneka kuti ambiri ankafuna kuphunzira choonadi moti sitinkavutika  kuyamba kuphunzira nawo Baibulo. Pamene zaka zitatu zinkatha, mpingo wa Surabaya unali ndi ofalitsa 75.”

Amishonale omwe ankakhala mumzinda wa Jakarta

Pa nthawi imeneyi, bambo wina yemwe anali Msilamu, dzina lake Azis, wochokera mumzinda wa Padang ku West Sumatra, analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi. Iye anapempha kuti akufuna munthu woti aziphunzira naye Baibulo. Bambo Azis anali ataphunzirapo Baibulo ndi apainiya ena a ku Australia cha m’ma 1930. Koma dziko la Japan litayamba kulamulira dziko la Indonesia, zinali zovuta kuti apitirize kuphunzira ndi apainiyawo. Ndiyeno tsiku lina, anapeza kabuku kofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Bamboyu analemba kuti: “Nditaona adiresi ya a Mboni za Yehova pakabukuko, ndinayambanso kufuna kuphunzira.” Pofuna kuthandiza bamboyu, abale a ku ofesi ya nthambi anatumiza woyang’anira dera wina, dzina lake Frans van Vliet, kumzinda wa Padang. M’baleyu atafika anazindikira kuti bambo Azis anali atalalikira a Nazar Ris, omwe nyumba yawo inali pafupi ndi nyumba ya bambo Azis. A Nazar Ris ankagwira ntchito m’boma ndipo ankakonda zinthu zauzimu. Azibambowa limodzi ndi mabanja awo anaphunzira choonadi n’kubatizidwa. Kenako M’bale Azis anakhala mkulu mumpingo. M’bale Nazar Ris anakhala mpainiya wapadera ndipo ana ake ambiri akupitirizabe kutumikira Yehova mwakhama.

M’bale Frans van Vliet ndi mchemwali wake Nel

Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Van Vliet anapita kukaona m’bale wina wachidatchi yemwe anali atasiya kusonkhana. M’baleyu ankakhala mumzinda wa Balikpapan, ku East Kalimantan ndipo ankagwira ntchito yokonza makina oyenga mafuta. Makinawa anali atawonongeka pa nthawi ya nkhondo. Tsiku lina M’bale Van Vliet anayenda ndi m’baleyu mu utumiki ndipo anamulimbikitsa kuti aziphunzira Baibulo ndi anthu amene ankachita chidwi ndi uthenga wathu. M’bale wachidatchiyu asanabwerere kwawo ku Netherlands anali atakhazikitsa kagulu ka ofalitsa ku Balikpapan.

Kenako mlongo wina yemwe anali atangobatizidwa kumene, dzina lake Titi Koetin, anasamukira mumzinda wa Banjarmasin ku South Kalimantan. Mlongoyu analalikira achibale ake omwe ndi a mtundu wa Adayaki ndipo ambiri anaphunzira choonadi. Ena mwa achibale ake anabwerera kumidzi ya ku Kalimantan ndipo anakhazikitsa magulu omwe patapita nthawi, anakhala mipingo yolimba.

 Anayamba Kusindikiza Mabuku M’Chiindoneziya

Abale atayamba kulalikira m’madera ambiri, pankafunikanso mabuku ambiri a Chiindoneziya. Choncho mu 1951, abale anamasulira buku lachingelezi lakuti, “Let God Be True.” Koma bungwe loona za malamulo a chiyankhulo m’dzikoli linasintha malamulo a kalembedwe ka mawu, bukuli lisanatuluke. Zimenezi zinachititsa kuti abale akonzenso buku limene anamasulira lija lisanatuluke. * Ndiyeno bukuli litatuluka, anthu owerenga Chiindoneziya anachita nalo chidwi kwambiri.

Mu 1953, ofesi ya nthambi inasindikiza magazini 250 a Nsanja ya Olonda m’Chiindoneziya. Pa nthawiyi panali patadutsa zaka 12 kuchokera pamene anasindikiza magazini ena a m’Chiindoneziya. Poyamba, magaziniyi inkakhala ya masamba 12 ndipo inkangokhala ndi nkhani zophunzira zokha. Koma patadutsa zaka zitatu, magaziniyi inayamba kukhala ya masamba 16. Kampani ina ndi imene inkasindikiza magaziniwa ndipo inkasindikiza magazini 10,000 mwezi uliwonse.

Magazini a Galamukani! anayamba kutuluka m’Chiindoneziya mwezi ndi mwezi kuyambira mu 1957. Chiwerengero cha magazini amene ankafalitsidwa chinawonjezeka kwambiri kufika pa 10,000. Koma pasanapite nthawi yaitali, mapepala osindikizira mabuku  anayamba kusowa m’dzikoli, moti sankagulitsidwa mwachisawawa. Choncho abale ankafunika kukhala ndi laisensi yoti azigula mapepalawa mosavutikira. Abalewa atapita kuboma kuti akapeze laisensiyo, mkulu wa boma amene anakumana naye anawauza kuti: “Ndimaona kuti magazini a Nsanja ya Olonda ndi abwino kwambiri. Ndikuthandizani kupeza laisensi kuti mupitirize kusindikiza magazini anu.”

^ ndime 1 Kuchokera m’chaka cha 1945, bungwe loona za malamulo a chiyankhulo ku Indonesia lasintha kawiri kalembedwe ka mawu a m’Chiindoneziya. Linachita zimenezi pofuna kusintha mmene Adatchi ankalembera mawu.