Yesu ananeneratu zimene zinkayenera kuchitika Yerusalemu akadzatsala pang’ono kuwonongedwa mu 70 C.E. Iye anati: ‘Anthu ambiri . . . adzadana. . . . Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.’ (Mat. 24:10, 12) Koma mosiyana ndi anthu amenewa, otsatira ake akanadziwika chifukwa cha chikondi. (Yoh. 13:35) Patapita nthawi, mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu achiheberi omwe ankakhala ku  Yerusalemu. M’kalatayi, anawayamikira chifukwa chakuti ankakondana ndipo anawalimbikitsa kuti apitirize kukondana.

Panopa tikuyembekezera kuti dziko loipa la Satanali liwonongedwa posachedwapa. Mofanana ndi mmene zinthu zinali m’nthawi ya atumwi, ifenso timakhala ndi anthu omwe amakonda ndalama, zosangalatsa, ndi odzikonda komanso sakonda Mulungu ndiponso anzawo. (2 Tim. 3:1-4) Ngakhale zili choncho, a Mboni za Yehovafe timakondana kwambiri padziko lonse lapansi. Choncho tiyeni tipitirize kulemekeza Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, pamene tikuyesetsa kukonda abale athu.