Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene a Mboni za Yehova akwanitsa kuchita m’chaka cha 2015 komanso mmene ntchito yawo yakhala ikuyendera ku Indonesia.

Lemba Lachaka cha 2016

Lemba la Aheberi 13:1 lili ndi mfundo yotilimbikitsa komanso yoyamikira zimene tikuchita.

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata imeneyi ikusonyeza mmene zinthu ngati webusaiti ya jw.org, JW Broadcasting, timashelefu tolalikirira komanso Msonkhano Wachigawo wa 2015 zathandizira anthu ambiri.

“Timakonda Kwambiri TV ya JW Broadcasting”

Kodi abale anachita zotani kuti akonze situdiyoyi?

Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira

Gulu lasintha zinthu zina pa nkhani ya zomangamanga kuti zithandize anthu ambiri kumanga Nyumba za Ufumu.

Kodi Ntchito Yomanga Ikuyenda Bwanji ku Warwick?

Dziwani mwachidule mmene ntchito yathu yomanga ikuyendera ku likulu la Mboni za Yehova.

Njira Imene Ikuthandiza Kulalikira Anthu Omwe Sapezeka Pakhomo

N’chiyani chinachititsa bambo Terry kukhulupirira kuti zimene anamva kwa Mboni za Yehova, linali yankho la pemphero lake?

Kuwala Kukuwonjezerekabe

M’chigawo chino, muona mmene Yehova akuthandizira anthu amene amamulambira.

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Kumayambiriro kwa chaka cha 2015 a Mboni za Yehova ku Madagascar ndi ku Indonesia anachita mwambo wotsegulira maofesi a nthambi m’mayiko awo.

Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri

M’chaka cha utumiki cha 2015, Mabaibulo a m’zinenero zokwana 16 anatulutsidwa.

Lipoti la Milandu

Padziko lonse, a Mboni za Yehova akupitirizabe kutsutsidwa ndi akuluakulu a boma komanso zipembedzo zina.

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Ndalama zimene Ken ankaponya m’kabokosi kake zinathandiza pa nthawi yomanga Nyumba ya Ufumu.

Africa

Kodi ndi njira zatsopano ziti zimene a Mboni za Yehova akugwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino?

North ndi South America

N’chifukwa chiyani mzimayi wina amachita kupita kumunda usiku kukaphunzira Baibulo atayatsa kandulo? N’chifukwa chiyani mfumu ina inkafuna kukumana ndi a Mboni? Nanga n’chiyani chinachititsa kuti munthu wina yemwe kale ankazunza a Mboni alire?

Ku Asia ndi ku Middle East

Zinthu ngati kumangidwa kapena kulumala sizilepheretsa anthu kulalikira za Ufumu.

Europe

Munthu woyankhula Chiromane, munthu yemwe ali m’ndende komanso mayi wina yemwe ankafuna kudzipha anasangalala atamva uthenga wabwino.

Oceania

Matebulo olalikirirapo, timashelefu tolalikirirapo, webusaiti ya jw.org komanso mavidiyo athu akuthandiza anthu ambiri kuti adziwe zimene Baiublo limaphunzitsa

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Indonesia

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zachidule zokhudza dziko, anthu komanso chikhalidwe cha anthu a ku Indonesia. Dzikoli ndi lomwe lili ndi zilumba zambiri padziko lonse lapansi.

Malonda a Zokometsera Chakudya

M’zaka za m’ma 1500, malonda a zokometsera chakudya ndi amene ankabweretsa ndalama m’mayiko ambiri.

Ndikufuna Kukayambira Apa

Apainiya olimba mtima ochokera ku Australia anapirira mavuto ambiri pamene ankagwira ntchito yolalikira koyamba ku Indonesia.

Njira Zimene Poyamba Ankagwiritsa Ntchito Polalikira

Kulalikira pa wailesi ndi m’madoko kumene a Mboni za Yehova ankachita, kunakhumudwitsa anthu amene ankadana ndi choonadi ku Indonesia.

Kunayambika Kagulu Kenakake ka Chipembedzo

Poyamba anthu a m’kaguluka ankatsatira mfundo zimene ankawerenga m’mabuku a Mboni za Yehova. Koma patapita nthawi, anayamba kuyendera maganizo awo.

Ankaona Kuti Kukhala pa Ubwenzi ndi Yehova N’kofunika Kwambiri

Gulu la anthu olusa linathyola chitseko cha nyumba ya a Thio Seng Bie akuona. Anthuwa anatenga katundu wina n’kusiya katundu amene mwiniwake ankaona kuti ndi wamtengo wapatali.

Ntchito Yolalikira Inabala Zipatso ku West Java

A Mboni anapitiriza kulalikira mosamala kwambiri pa nthawi imene mabuku awo analetsedwa.

Ulamuliro Wankhanza wa Boma la Japan

Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, a Mboni ena anapeza njira yodulira makadi mosalimbana ndi boma la Japan kapenanso mosalowerera ndale.

Mpainiya Wopanda Mantha

M’bale André Elias anatumikira kwa zaka 60 ndipo anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankafunsidwa mafunso komanso kuopsezedwa.

Amishonale Anayamba Kufika ku Indonesia

Amishonale oyambirira kufika m’dzikoli anathandiza kupititsa patsogolo ntchito yolalikira mofulumira kwambiri.

Ntchito Yolalikira Inafika Mpaka ku Zilumba Zakum’mawa

Kodi atsogoleri achipembedzo anakwanitsanso kulepheretsa ntchito yolalikira?

Amishonale Enanso Anafika

Chapakatikati pa zaka za m’ma 1970, zinthu zinayamba kusintha moti zinali zovuta kulalikira uthenga wabwino.

Ankachita Zinthu Ngati Sara Weniweni

Mlongo Titi Koetin ankalemekeza kwambiri mwamuna wake ndipo zimenezi zinathandiza kwambiri banja lake.

Msonkhano Wosaiwalika

Msonkhano wa mayiko wa mutu wakuti, “Uthenga Wabwino Wosatha” wa mu 1963, unachitikabe ngakhale kuti abale anakumana ndi mavuto osiyanasiyana.

Ndinapulumuka Pamene Chipani cha Chikomyunizimu Chinkafuna Kulanda Boma

Anali atakumbiratu manda a M’bale Ronald Jacka.

Anachita Upainiya Wapadera kwa Zaka 50

M’chaka cha 1964 ku West Papua, m’busa wina wa tchalitchi cha Chipulotesitanti anayankhula mwaukali kuti: “Ndithetsa gulu la Mboni za Yehova ku Manokwari kuno.” Kodi iye anachitadi zimenezi?

Poyamba Anali Mtsogoleri wa Zigawenga Koma Kenako Anakhala Nzika Yabwino

Mkulu wa ofufuza milandu anafunsa a Mboni za Yehova kuti: Kodi a Mboni za Yehova amachita chiyani kwenikweni ku Indonesia kuno?

Anatsimikiza Mtima Kuti Sabwerera M’mbuyo

N’chiyani chinachititsa anthu ena kunena kuti, “A Mboni za Yehova ali ngati misomali”?

Sanasiye Kusonkhana

A Mboni za Yehova ataloledwanso kuti azigwira ntchito yawo mwaufulu, mkulu wina wa boma ananena kuti: “Sichikalatachi chimene chikukupatsani ufulu wopembedza.”

Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto

A Mboni za Yehova akuthandiza abale mwamsanga chivomezi chitawononga tauni ya Gunungsitoli ku Indonesia.

Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira

Daniel Lokollo amakumbukira mmene olondera ndende anamuzunzira.

Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira Malangizo

Kumenyana kwa Asilamu ndi Akhristu ku Indonesia kunabweretsa mavuto kwa a Mboni za Yehova.

Ntchito Yathu Inayambanso Kuyenda Bwino

Ntchito yathu itavomerezedwanso, panachitika zinthu zikuluzikulu zitatu zomwe zinathandiza anthu ambiri.

Abale Ankalengeza za Yehova Molimba Mtima

Kodi a Mboni za Yehova anachita zotani kuti zinthu ngati chikhalidwe ndi zizolowezi zoipa zisawalepheretse kulalikira molimba mtima?

Ofesi ya Nthambi Yomwe Ili M’mwamba Kwambiri

Abale ndi alongo olalikira kumadera ofunika ofalitsa ambiri akhala akufunafuna gawo la anthu ofuna kudziwa choonadi ndipo alipeza.

“Yehova Anatichitira Zinthu Zoposa Zimene Tinkayembekezera”

Mpingo wa m’mudzi wa Tugala Oyo, ku Indonesia, unadalitsidwa kwambiri.

Tinasangalala Titadziwa Kuti Ndife Pachibale

Atsikana awiri apachibale m’dziko la Indonesia anawasiyanitsa wina ataperekedwa kuti akaleredwe ndi banja lina koma kuphunzira Baibulo kunawathandiza kuti akumanenso.

Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo mu 1916

Zimene zinatika kumepeto kwa chaka cha 1916 zinali zofunika kwambiri kwa Ophunzira Baibulo.

Ziwerengero Zonse za 2015

Kodi tinachita zotani komanso tinagwiritsa ntchito ndalama zingati polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?

Mwambo wa Chikumbutso—Lachisanu pa 3 April, 2015

Ntchito yoitanira anthu kumwambo wa Chikumbutso yomwe abale ndi alongo anagwira kwa milungu 4 inayenda bwino kwambiri.