Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mudzatani pa Nthawi ya Chilala?

Kodi Mudzatani pa Nthawi ya Chilala?

Nthawi zonse tiyenera kukhulupirira komanso kudalira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, kukhulupirira Yehova kumatithandiza kumudalira kuti atiteteza komanso kutisamalira. (Sal. 23:1, 4; 78:22) Pamene tikuyandikira mapeto a dziko loipali, Satana walusa kwambiri moti akuchita chilichonse kuti atiukire. (Chiv. 12:12) Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisagonje?

ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI MUDZATANI PA NTHAWI YA CHILALA? NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  1. Kodi tingakhale bwanji ngati “mtengo” wotchulidwa pa Yeremiya 17:8?

  2. Kodi “kutentha” kwina kungakhale chiyani?

  3. Kodi ‘mtengowu’ unakhudzidwa bwanji, nanga n’chifukwa chiyani?

  4. Kodi Satana amafuna kuwononga chiyani?

  5. Kodi tingafanane bwanji ndi munthu amene wakhala akukwera ndege kwa nthawi yaitali?

  6. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kudalira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zingakhale zovuta nthawi zina?

  7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kudalira mfundo za m’Baibulo ngakhale pamene anthu ena akutinyoza?