4:6-26, 39-41

Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti alalikire mwamwayi?

  • 4:7​—Iye anayamba n’kupempha madzi m’malo moyamba ndi kumufotokozera za Ufumu wa Mulungu kapena kumudziwitsa kuti iyeyo ndi Mesiya

  • 4:9​—Yesu sanachite tsankho kwa mayi wachisamariya chifukwa cha mtundu wake

  • 4:9, 12​—Mayiyo atayambitsa nkhani zimene zikanachititsa kuti asemphane maganizo, Yesu anapewa nkhanizo mwanzeru n’kupitirizabe kukambirana naye nkhani yofunikirayo.​—cf 77 ¶3

  • 4:10​—Iye anayamba ndi chitsanzo cha zimene mayiyo ankachita tsiku ndi tsiku

  • 4:16-19​—Ngakhale kuti mayiyu anali wachiwerewere, Yesu ankamulemekezabe

Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kufunika kolalikira mwamwayi?