NSANJA YA OLONDA

Funso: Kodi angelo alipodi?

Lemba: Sal. 103:20

Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza angelo ndiponso mmene amatithandizira masiku ano.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi mumaona kuti sayansi imatsutsana ndi Baibulo?

Lemba: Yes. 40:22

Zoona Zake: Zimene Baibulo limanena pa nkhani za sayansi n’zolondola.

KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KUMISONKHANO (inv)

Munganene Kuti: Ndikukuitanirani kumisonkhano yathu kuti mudzamvetsere nkhani yochokera m’Baibulo. Idzakambidwa ku Nyumba ya Ufumu omwe ndi malo athu olambirira. [Perekani kapepalako ndipo musonyezeni nthawi komanso malo a misonkhanoyo. Muuzeninso mutu wa nkhani ya mlungu umenewo.]

Funso: Kodi munayamba mwapitapo ku Nyumba ya Ufumu? [Ngati n’zotheka muonetseni vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.