Masomphenya a Ezekieli onena za kachisi analimbitsa mitima ya Aisiraeli omwe anali ku ukapolo ndipo anatsimikiza kuti maulosi onena zoti adzabwerera kwawo adzakwaniritsidwa. Anthu amene Yehova anawadalitsa ankaona kuti kulambira koyera n’kofunika kwambiri.

Masomphenyawa anasonyeza kuti Aisiraeli azidzachita zinthu mwadongosolo, mogwirizana komanso adzakhala otetezeka

47:7-14

  • Dziko labwino lokhala ndi zakudya zochuluka

  • Banja lililonse linali ndi cholowa

Malo asanagawidwe kwa anthu, anaika padera gawo lina la malowo monga “chopereka” kwa Yehova

48:9, 10

Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimaika kulambira Yehova pamalo oyamba? (w06 4/15 27-28 ¶13-14)