CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 42-45
Kulambira Koyera Kunabwezeretsedwa
Masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi anatsimikizira Ayuda okhulupirika omwe anali ku ukapolo kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa. Komanso anawakumbutsa mfundo zapamwamba za Yehova zokhudza kulambira koyera.
Ansembe ankayenera kuphunzitsa anthu mfundo za Yehova
Fotokozani zitsanzo zosonyeza mmene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru watithandizira kuti tizidziwa kusiyana pakati pa chinthu chodetsa ndi choyera. (kr 110-117)
Anthu ankathandiza atsogoleri awo
Kodi tingathandize akulu mumpingo m’njira ziti?