Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  September 2017

September 4-10

Ezekieli 42-45

September 4-10
 • Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Kulambira Koyera Kunabwezeretsedwa”: (10 min.)

  • Ezek. 43:10-12​—Masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi anathandiza Ayuda omwe anali ku ukapolo kuti alape komanso anawatsimikizira kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa pamalo ake okwezeka (w99 3/1 8 ¶3; it-2 1082 ¶2)

  • Ezek. 44:23​—Ansembe ankafunika kuphunzitsa anthu kuti adziwe “kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi choyera”

  • Ezek. 45:16​—Anthu ankayenera kuthandiza atsogoleri amene Yehova anawasankha kuti aziwatsogolera (w99 3/1 10 ¶10)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Ezek. 43:8, 9​—Kodi Aisiraeli anadetsa bwanji dzina la Mulungu? (it-2 467 ¶4)

  • Ezek. 45:9, 10​—Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amamutumikira azichita chiyani nthawi zonse? (it-2 140)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ezek. 44:1-9

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU