Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  September 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muziwaphunzitsa Kuti Azitumikira Yehova Mosalekeza

Muziwaphunzitsa Kuti Azitumikira Yehova Mosalekeza

Nthawi zambiri, ofalitsa atsopano amene aphunzitsidwa kuyambira pachiyambi kuti azigwira nawo ntchito yolalikira mwakhama, amadzakhala ofalitsa aluso. (Miy. 22:6; Afil. 3:16) Malangizo otsatirawa akusonyeza mmene tingathandizire wophunzira kuti azigwira bwino ntchito yolalikira:

  • Wophunzira wanu akavomerezedwa kukhala wofalitsa, yambani nthawi yomweyo kumuphunzitsa. (km 8/15 1) Muthandizeni kuti aziona kufunika kogwira ntchito yolalikira mlungu uliwonse. (Afil. 1:10) Muzilankhula zabwino za anthu a m’gawo lanu. (Afil. 4:8) Mulimbikitseni kuti azilowa mu utumiki ndi woyang’anira kagulu komanso ofalitsa ena n’cholinga choti apeze luso.​—Miy. 1:5; km 10/12 6 ¶3

  • Wophunzira wanu akabatizidwa, musasiye kumulimbikitsa komanso kumuthandiza mmene angachitire zinthu mu utumiki, makamaka ngati simunamalize kuphunzira naye buku lakuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani.’​km 12/13 7

  • Mukayenda limodzi ndi wofalitsa watsopano mu utumiki, muzigwiritsa ntchito ulaliki wosavuta. Mukaona mmene akulalikirira, muzimuyamikira. Kenako mufotokozereni mfundo zina zimene zingamuthandize kuti azilalikira mogwira mtima.​—km 5/10 7