Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akuitanira anthu kumisonkhano ku Cook Islands

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU September 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Nsanja ya Olonda ndiponso kuphunzitsa choonadi chokhudza Baibulo ndi sayansi. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kulambira Koyera Kunabwezeretsedwa

Masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi anatsimikizira Ayuda okhulupirika omwe anali ku ukapolo kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

N’chifukwa Chiyani Mumaona Kuti Kulambira Koyera N’kofunika?

Masiku ano kulambira koyera kukupita patsogolo kwambiri. Kodi inuyo nthawi zonse mumasonyeza kuyamikira mwayi wodziwa Yehova Mulungu komanso kumutumikira?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Aisiraeli Omwe Anachoka ku Ukapolo Analandira Madalitso

Masomphenya onena za kachisi omwe Ezekieli anaona, anasonyeza kuti aisiraeli azidzachita zinthu mwadongosolo, mogwirizana komanso adzakhala otetezeka.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kukhala Okhulupirika kwa Yehova Kumabweretsa Madalitso

Nkhani ya anyamata atatu Achiheberi ingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova Mulungu

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala Okhulupirika Mukakumana ndi Mayesero

Yesu Khristu anakhalabe okhulupirika pamene anakumana ndi mayesero. Kodi anthu opanda ungwiro angakhalebe okhulupirika kwa Mulungu pamene akumana ndi mayesero?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala Okhulupirika Wachibale Wanu Akachotsedwa

Wachibale wathu akachotsedwa mumpingo, mwina zingativute kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe okhulupirika?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Mupitiriza Kutumikira Yehova Mosalekeza?

Danieli anatumikira Yehova mosalekeza. Sanalole chilichonse kumulepheretsa kuchita zimenezi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muziwaphunzitsa Kuti Azitumikira Yehova Mosalekeza

Wophunzira wanu akavomerezedwa kukhala wofalitsa, yambani nthawi yomweyo kumuphunzitsa. Muthandizeni wophunzirayo kuti azigwira ntchito yolalikira mwakhama.