Kutsatira chilamulo cha Yehova kumatanthauza kumvera chilichonse chimene Yehova amatiuza. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe ankadalira Yehova komanso kutsatira chilamulo chake ngati mmene wamasalimo anachitira.

Kutsatira chilamulo cha Yehova n’kumene kumatichititsa kukhalabe osangalala

119:1-8

Yoswa ankadalira kwambiri Yehova akamachita zinthu. Ankadziwa kuti ankayenera kumadalira Yehova ndi mtima wake wonse kuti akhale wosangalala komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino

Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima tikamakumana ndi mavuto

119:33-40

Yeremiya anali wolimba mtima komanso ankadalira Yehova pamene ankakumana ndi mavuto. Iye ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo sanasiye kuchita utumiki wake

Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima

119:41-48

Paulo sankachita mantha kulalikira uthenga wochokera kwa Mulungu kwa munthu aliyense. Pamene ankalalikira uthenga wabwino kwa Bwanamkubwa Felike, iye ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza

Kodi ndi pa nthawi iti pamene ndingasonyeze kulimba mtima ndikamalalikira?

  • Kusukulu

  • Kuntchito

  • Achibale

  • Anthu Ena