• Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • ‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’”: (10 min.)

  • Sal. 119:1-8—Kutsatira chilamulo cha Mulungu n’kumene kumatichititsa kukhalabe osangalala (w05 4/15 10 ndime 3-4)

  • Sal. 119:33-40—Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima tikamakumana ndi mavuto (w05 4/15 13 ndime 12)

  • Sal. 119:41-48—Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima (w05 4/15 13 ndime 13-14)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 119:71—Kodi kukumana ndi mavuto kuli ndi ubwino wotani? (w06 9/1 14 ndime 4)

  • Sal. 119:96—Kodi mawu akuti “zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire” akutanthauza chiyani? (w06 9/1 14 ndime 5)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 119:73-93

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyi. Limbikitsani ofalitsa kuti alembe ulaliki wawowawo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU