Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  September 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 135-141

Tinapangidwa Modabwitsa Kwambiri

Tinapangidwa Modabwitsa Kwambiri

Davide ankaganizira za makhalidwe a Mulungu omwe amaonekera m’zinthu zimene analenga. Zimenezi zinachititsa kuti azitumikira Yehova ndi mtima wonse.

Davide atayamba kuganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga, anayamba kutamanda Yehova

139:14

  • “Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa”

139:15

  • “Mafupa anga sanali obisika kwa inu pamene munali kundipanga m’malo obisika, pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri padziko lapansi”

139:16

  • “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu”