• Nyimbo Na. 59 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Tinapangidwa Modabwitsa Kwambiri”: (10 min.)

  • Sal. 139:14—Tikamaganizira zimene Yehova amachita, timayamba kumukonda kwambiri komanso kumuyamikira (w07 6/15 21 ndime 1-4)

  • Sal. 139:15, 16—Majini komanso maselo omwe amapezeka m’thupi lathu amasonyeza kuti Yehova ndi wamphamvu komanso wanzeru (w07 6/15 22-23 ndime 7-11)

  • Sal. 139:17, 18—Anthu ndi osiyana kwambiri ndi zinyama chifukwa amatha kulankhula komanso kuganiza (w07 6/15 23 ndime 12-13; w06 9/1 16 ndime 8)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 136:15—Kodi vesili likutithandiza bwanji kumvetsa nkhani yomwe inatchulidwa m’buku la Ekisodo? (w15 11/1 4 ndime 1; it-1-E 783 ndime 5)

  • Sal. 141:5—Kodi Mfumu Davide anazindikira chiyani? (w15 4/15 31 ndime 1)

  • Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 139:1-24

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) wp16.5 16

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) wp16.5 16—Muitanireni kumisonkhano yathu

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) fg phunziro 8 ndime 8—Thandizani wophunzira wanu kuti azigwiritsa ntchito zimene waphunzira

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 57

 • Zinthu Zimene Tiyenera Kupewa Tikamachititsa Phunziro la Baibulo”: (15 min.) Mukamaliza kukambirana nkhaniyi, onetsani vidiyo yosonyeza zinthu zoyenera komanso zosayenera kuchita tikamaphunzira Baibulo ndi munthu pogwiritsa ntchito buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa patsamba 31 ndime 7. Limbikitsani ofalitsa onse kuti azitsatira m’mabuku awo pamene vidiyoyi ikuonetsedwa. Pomaliza kumbutsani abale ndi alongo onse omwe amapatsidwa nkhani m’sukulu kuti ngati atamapewa kuchita zinthu zosayenera zomwe takambirana m’nkhaniyi, akhoza kumamaliza nkhani zawo pa nthawi yake.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 7 ndime 1-14.

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero