CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Muzitsanzira Yesu pa Nkhani Yochitira Ena Chifundo”: (10 min.)

  • Yoh. 11:23-26​—Yesu analimbikitsa Marita (“Ndikudziwa kuti adzauka” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:24, nwtsty; “Ine ndine kuuka ndi moyo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:25, nwtsty)

  • Yoh. 11:33-35​—Yesu anamva chisoni kwambiri ataona Mariya komanso anthu ena akulira (“kulira,” “anadzuma . . . ndi kumva chisoni,” “povutika mumtima” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:33, nwtsty; anagwetsa misozi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:35, nwtsty)

  • Yoh. 11:43, 44​—Yesu anawachitira chifundo n’kuwathandiza

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yoh. 11:49​—Kodi ndi ndani amene anasankha Kayafa kuti akhale mkulu wa ansembe, nanga anakhala paudindowu kwa nthawi yaitali bwanji? (“mkulu wa ansembe” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:49, nwtsty)

  • Yoh. 12:42​—N’chifukwa chiyani Ayuda ena ankachita mantha kuvomereza kuti Yesu ndi Khristu? (“olamulira,” “angawachotse musunagoge” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 12:42, nwtsty)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yoh. 12:35-50

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsirani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba.

 • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

 • Nkhani: (Osapitirira 6 min.) w13 9/15 32​—Mutu: N’chifukwa Chiyani Yesu Analira Asanaukitse Lazaro?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 141

 • Yesu Ndi “Kuuka ndi Moyo” (Yoh. 11:25): (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani mbali ina ya vidiyo yakuti, “Mulungu Anamuika Kukhala Ambuye ndi Khristu”​—Mbali Yachiwiri. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi nkhani imeneyi ikutithandiza bwanji kudziwa kuti Yesu anali wachifundo kwambiri? Kodi Yesu ndi “kuuka ndi moyo” m’njira yotani? Kodi Yesu adzachita zozizwitsa zotani m’tsogolo?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 8

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 148 ndi Pemphero