GALAMUKANI!

Funso: N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera ngozi zadzidzidzi?

Lemba: Miy. 27:12

Perekani Magaziniyo: Magazini iyi ikufotokoza zimene tingachite ngozi isanachitike, ikamachitika komanso pambuyo poti yachitika.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi timasonyeza bwanji kuti timakonda Mulungu?

Lemba: 1 Yoh. 5:3

Zoona Zake: Timasonyeza kuti timakonda Mulungu tikamamvera malamulo ake.

KODI N’ZOONADI KUTI AKUFA ADZAUKA? (T-35)

Funso: Chaka chilichonse, anthu ambiri padziko lonse amachita miyambo yolemekeza akufa. Kodi n’zotheka kudzaonananso ndi achibale komanso anzathu amene anamwalira?

Lemba: Mac. 24:15

Perekani Kapepalako: Kapepala aka kakufotokoza mmene chiyembekezo choti akufa adzauka chingatithandizire. [Ngati n’kotheka, muonetseni vidiyo yakuti Kodi Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo?]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito