11:2

Padzakhala mafumu 4 ochokera mu ufumu wa Perisiya. Mfumu ya nambala 4 “idzaukira ufumu wa Girisi ndi mphamvu zake zonse.”

  1. Koresi Wamkulu

  2. Kambisesi II

  3. Dariyo I

  4. Sasta I (ena amati ndi Mfumu Ahasiwero amene anakwatira Esitere)

11:3

Mfumu yamphamvu ya Girisi inayamba kulamulira dera lalikulu kwambiri.

  • Alekizanda Wamkulu

11:4

Akuluakulu 4 a asilikali a Alekizanda anagawana ufumu wa Girisi.

  1. Kasanda

  2. Lasamekasi

  3. Selukasi I

  4. Tolemi I