Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  October 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOWELI 1-3

“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenera”

“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenera”

2:28, 29

Akhristu odzozedwa amagwira ntchito yonenera. Iwo amauza ena za “zinthu zazikulu za Mulungu” ndipo amalengeza “uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mac. 2:11, 17-21; Mat. 24:14) Ankhosa zina amathandiza odzodzedwawa pogwira nawo ntchito yolalikira.

2:32

Kodi ‘kuitana pa dzina la Yehova’ kumatanthauza chiyani?

  • Kudziwa dzinalo

  • Kulemekeza dzinalo

  • Kudalira komanso kukhulupirira mwiniwake wa dzinalo

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingathandize bwanji Akhristu odzozedwa omwe amagwira ntchito yonenera?’