Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  October 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse

Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse

Moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali. Zimene timachita tsiku ndi tsiku zimasonyeza ngati timayamikira mphatsoyi kapena ayi. Monga Mboni za Yehova, timayesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu zathu komanso luso lathu potumikira Yehova, yemwe anatipatsa moyo. (Sal. 36:9; Chiv. 4:11) Komabe nkhawa za tsiku ndi tsiku zimene timakhala nazo zingasokoneze zolinga zathu zofuna kutumikira Yehova. (Maliko 4:18, 19) Choncho tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyesetsa kuchita zonse zimene ndingathe potumikira Yehova? (Hos. 14:2) Kodi ntchito imene ndimagwira ikundilepheretsa kuchita zambiri? Kodi zolinga zanga n’zotani? Kodi ndingatani kuti ndizichita zambiri mu utumiki?’ Ngati mukuona kuti pali zina zimene mukufunikira kusintha, pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Musamakayikire kuti kutumikira Yehova nthawi zonse kudzakuthandizani kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala.​—Sal. 61:8.

Kodi inuyo mumapereka luso lanu kwa ndani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO LUSO LANU KUTUMIKIRA YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani tinganene kuti si nzeru kugwiritsa ntchito luso lathu pa zinthu za m’dziko la Satanali? (1 Yoh. 2:17)

  • Kodi anthu amene amachita zonse zimene angathe potumikira Yehova amapeza madalitso otani?

  • Kodi mungathe kugwiritsa ntchito luso lanu pochita mautumiki osiyanasiyana ati?