Kodi mumafuna kukhala wokhulupirika mukakumana ndi mayesero ngati mmene Danieli anachitira? Danieli ankaphunzira Mawu a Mulungu kuphatikizapo maulosi ozama mwakhama. (Dan. 9:2) Nanunso mukamaphunzira Baibulo mwakhama, mudzakhalabe okhulupirika. Mudzayamba kukhulupirira kwambiri kuti zimene Yehova walonjeza zidzachitikadi. (Yos. 23:14) Kuphunzira Baibulo mwakhama kungakuthandizeninso kuti muzikonda kwambiri Mulungu ndiponso kuti muzichita zoyenera. (Sal. 97:10) Koma kodi mungayambire pati? Taganizirani mafunso otsatirawa.

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kuphunzira? Muzikonzekera nkhani zonse zimene mukaphunzire kumisonkhano yampingo. Kuti muzipindula ndi kuwerenga Baibulo kwa mlungu uliwonse, muzifufuza mfundo zimene simukuzimvetsa bwino. Ena amasankha kuti aphunzire zinthu monga maulosi a m’Baibulo, makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, maulendo a umishonale a mtumwi Paulo kapenanso zokhudza chilengedwe. Ngati muli ndi funso pa nkhani inayake, muzililemba n’cholinga choti mudzalifufuze pa ulendo wotsatira.

  • Kodi ndingapeze kuti mfundo za nkhani imene ndikufuna kuphunzira? Onerani vidiyo yakuti Zinthu Zotithandiza Pofufuza Chuma cha M’mawu a Mulungu kuti mupeze mfundo zina. Ndiyeno tayesani kufufuza zokhudza maulamuliro amphamvu padziko lonse oimiridwa ndi zilombo zotchulidwa mu Danieli chaputala 7.

  • Kodi ndiziphunzira kwa nthawi yaitali bwanji? Mukamaphunzira nthawi zonse mudzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mukhoza kuyamba ndi kumaphunzira kwa kanthawi kochepa kenako mungamawonjezere pang’onopang’ono nthawi yophunzirayo. Kuphunzira Mawu a Mulungu tingakuyerekezere ndi kufufuza chuma chobisika chimene ukayamba kuchipeza, umafunitsitsa kufufuzabe. (Miy. 2:3-6) Mukamachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Mawu a Mulungu ndipo kuphunzira Baibulo kudzangokhala ngati mbali ya moyo wanu.​—1 Pet. 2:2.

KODI ZILOMBO ZOTCHULIDWA MU DANIELI CHAPUTALA 7 ZIMAIMIRA CHIYANI?

FUNSO LOWONJEZERA:

Kodi lemba la Danieli 7:8, 24 linakwaniritsidwa bwanji?

ZOTI MUDZAFUFUZE ULENDO WOTSATIRA:

Kodi zilombo zotchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 13 zimaimira chiyani?