Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akugawira kapepala kakuti Akufa Adzauka? ku Tuvalu

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU October 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Galamukani! ndiponso kuphunzitsa choonadi chokhudza zimene tingachite kuti tizisonyeza kuti timakonda Mulungu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Ulosi wa Danieli Unaneneratu Nthawi Imene Mesiya Adzafike

Muchaputala 9 cha Danieli muli ulosi wosonyeza nthawi imene Mesiya adzafike. Kodi ndi zochitika zinanso ziti zomwe ulosiwu umafotokoza?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingatani Kuti Tiziphunzira Malemba Mwakhama

Kuphunzira Baibulo mwakhama kungakuthandizeni kukhalabe okhulupirika mukakumana ndi mayesero. Koma kodi mungayambire pati kuphunzira?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Ananeneratu Zokhudza Mafumu a Mtsogolo

Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Danieli kuti alosere za mphamvu ndi kutha kwa maulamuliro komanso mafumu a mtsogolo.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Mumasangalala ndi Chikondi Chokhulupirika Ngati Mmene Yehova Amachitira?

N’chiyani chimatithandiza kuti tikhale ndi chikondi chokhulupirika? Kodi chitsanzo cha Hoseya komanso mkazi wake wosakhulupirika dzina lake Gomeri, chikutiphunzitsa chiyani?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzipereka Zinthu Zabwino Kwambiri kwa Yehova

Yehova amasangalala ndi nsembe zathu zabwino ndipo amatidalitsa. Kodi Yehova amaona kuti nsembe yabwino kwambiri imene tingamupatse ndi iti?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse

Moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali. Timayesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu zathu komanso luso lathu potumikira Yehova, yemwe anatipatsa moyo.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenera”

Kodi tingathandize bwanji Akhristu odzozedwa omwe amagwira ntchito yonenera?