Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 22-26

“Phunzitsa Mwana M’njira Yomuyenerera”

“Phunzitsa Mwana M’njira Yomuyenerera”

Buku la Miyambo lili ndi malangizo abwino amene angathandize makolo. Mofanana ndi mfundo yakuti kuwongola mtengo n’kulinga uli waung’ono, tikamaphunzitsa bwino ana nthawi zambiri amapitiriza kutumikira Yehova akakula.

22:6

  • Kuphunzitsa bwino ana kumafuna nthawi yambiri komanso khama

  • Makolo ayenera kukhala chitsanzo chabwino ndipo ayenera kuphunzitsa, kulangiza, kulimbikitsa ndiponso nthawi zina kupereka chilango kwa ana awo

22:15

  • Mawu amene anawamasulira kuti ‘kulanga’ mulembali amatanthauzanso kuphunzitsa ndiponso kulangiza mwana mwachikondi n’cholinga choti asinthe maganizo ndiponso mtima wake

  • Ana amafunika kulangizidwa m’njira zosiyanasiyana