Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  October 2016

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?

Popeza kuti chisautso chachikulu chayandikira, tiyenera kugwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. (Miy. 24:11, 12, 20) Tikhoza kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo komanso kupita pawebusaiti yathu pogwiritsa ntchito makadi odziwitsa anthu za jw.org. Makadiwa amakhala ndi kachidindo kothandiza anthu kuti apite pawebusaitiyi n’kupempha kuti aziphunzira Baibulo. Kachidindoka kamawathandizanso kuti aonere vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Anthu ena safuna kulandira mabuku athu koma angafune kupita pawebusaiti yathu. Choncho ndi bwino kuwapatsa makadiwa. Komabe si bwino kupatsa makadiwa anthu amene alibe chidwi.

Mukhoza kugawira makadiwa kwa anthu amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku. Mungayambe ndi kunena kuti: “Ndili ndi khadi limene ndikufuna ndikupatseni. Khadili lingakuthandizeni kupita pawebusaiti yaulere yomwe ili ndi nkhani komanso mavidiyo osiyanasiyana.” (Yoh. 4:7) Popeza kuti makadiwa ndi aang’ono, simungavutike kuwanyamula kulikonse kumene mungapite n’kumagawira anthu omwe mwakumana nawo.