Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  October 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 1-6

“Khulupirira Yehova ndi Mtima Wako Wonse”

“Khulupirira Yehova ndi Mtima Wako Wonse”

Yehova ndi woyenera kuti tizimukhulupirira ndi mtima wonse. Tanthauzo la dzina lake limatithandiza kukhulupirira kuti iye akhoza kukwaniritsa malonjezo ake onse. Kupemphera kungatithandizenso kumukhulupirira. Chaputala 3 cha Miyambo chimatitsimikizira kuti tikamadalira Yehova, ‘adzawongola njira zathu zonse.’

Munthu amene amadalira nzeru zake . . .

3:5-7

  • amasankha zochita popanda kupempha kaye Yehova kuti amuthandize

  • amatsatira maganizo ake kapena a anthu am’dzikoli

Munthu amene amadalira Yehova . . .

  • amaphunzira Baibulo, kuganizira zimene amaphunzirazo ndiponso kupemphera kuti azilimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova

  • akamasankha zochita amafufuza mfundo za m’Baibulo kuti adziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo

KODI INEYO NDIMASANKHA BWANJI ZOCHITA?

CHOYAMBA: Ndimasankha zimene ineyo ndikuona kuti ndi zanzeru

CHOYAMBA: Ndimapemphera ndiponso kuphunzira Baibulo kuti ndidziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo

CHACHIWIRI: Ndimapempha Yehova kuti adalitse zimene ndasankhazo

CHACHIWIRI: Ndimasankha zimene zikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo