Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 17-21

Yesetsani Kukhala Mwamtendere ndi Ena

Yesetsani Kukhala Mwamtendere ndi Ena

Sikuti zimangochitika zokha kuti anthu a Yehova azikhala mwamtendere. Iwo akhoza kusemphana maganizo ndipo nthawi zina zimakhala zovuta kuti asakwiyirane. Koma malangizo a m’Baibulo amawathandiza kwambiri kuti akhazikitsenso mtendere.

Akhristu akasemphana maganizo amayesetsa kukhala mwamtendere ndipo . . .

19:11

  • amakhala odekha

18:13, 17

  • amayesetsa kuti adziwe nkhani yonse asanachite chilichonse

17:9

  • amasonyeza chikondi pokhululukira munthu amene wawalakwira