Ndemanga zabwino zimalimbikitsa mpingo komanso zimathandiza anthu omwe amazipereka. (Miy. 15:23, 28; Aroma 14:19) N’chifukwa chake tiyenera kumayesetsa kupereka ndemanga pamsonkhano uliwonse. Komabe sikuti tingapatsidwe mwayi woyankha nthawi iliyonse imene takweza mkono. Choncho tingachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo.

Ndemanga yabwino imakhala . . .

  • yosavuta, yomveka bwino komanso yachidule. Nthawi zambiri ikhoza kukhala yosapitirira masekondi 30

  • imene mwaifotokoza m’mawu anuanu

  • imene sikungobwereza zimene anthu ena ayankha kale

Ngati ndinu woyamba kuyankha funso linalake, . . .

  • mungoyankha funsolo mwachidule popanda kufotokoza zambiri

Ngati funso layankhidwa kale, mukhoza . . .

  • kusonyeza mmene lemba lina la mundimeyo likugwirizanira ndi mfundo za mundimeyo

  • kufotokoza mmene mfundozo zingatithandizire

  • kufotokoza mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo

  • kufotokoza mwachidule chitsanzo chogwirizana ndi mfundo yaikulu ya mundimeyo