ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

Kodi nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali chifukwa chiyani? Imathandiza anthu kuti asamachite zinthu zoipa komanso imateteza moyo wawo. Imawathandizanso kuti akhale ndi khalidwe labwino ndiponso kuti azilankhula zabwino.

Nzeru imathandiza munthu kuti asakhale wodzikuza

16:18, 19

  • Munthu wanzeru amazindikira kuti Yehova ndi amene amapereka nzeru

  • Anthu amene zinthu zikuwayendera bwino komanso omwe apatsidwa udindo winawake ayenera kusamala kwambiri kuti asakhale onyada kapena odzikuza

Nzeru imathandiza munthu kuti azilankhula zolimbikitsa

16:21-24

  • Munthu wanzeru amayesetsa kuzindikira zinthu zabwino zimene ena amachita ndipo amalankhula zabwino zokhudza anthuwo

  • Mawu anzeru amakhala olimbikitsa ndiponso okoma ngati uchi, osati aukali kapena oyambitsa mikangano