Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO OCTOBER 2016

October 10-16

MIYAMBO 7-11

October 10-16
 • Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Mtima Wako Usapatuke”: (10 min.)

  • Miy. 7:6-12—Nthawi zambiri anthu opanda nzeru amachita zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova (w00 11/15 29-30)

  • Miy. 7:13-23—Munthu akasankha zinthu mopanda nzeru akhoza kukumana ndi mavuto aakulu (w00 11/15 30-31)

  • Miy. 7:4, 5, 24-27—Tikakhala anzeru komanso omvetsa zinthu tidzapewa mavuto ambiri (w00 11/15 29, 31)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Miy. 9:7-9—Kodi zimene timachita tikapatsidwa malangizo zimasonyeza kuti ndife anthu otani? (w01 5/15 29-30)

  • Miy. 10:22—Kodi ndi madalitso ati amene Yehova akutipatsa masiku ano? (w06 5/15 26-30 ndime 3-16)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Miy. 8:22-36; 9:1-6

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 83

 • Zimene Achinyamata Anzanu Amanena—Foni Zam’manja (Miy. 10:19): (15 min.) Nkhani yokambirana. Poyamba, onetsani vidiyo yakuti, Zimene Achinyamata Anzanu Amanena—Foni Zam’manja. Kenako kambiranani nkhani ya pa jw.org/ny yakuti, “Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?” Fotokozani bwino mfundo zomwe zili pakamutu kakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Nkhani ya Mameseji.”

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 8 ndime 17-27 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 75.

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 152 ndi Pemphero

  Kumbukirani: Muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.