Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akuitanira anthu kumisonkhano

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU October 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Mfundo zokuthandizani pogawira Galamukani!, kapepala koitanira anthu kumisonkhano ndiponso mfundo ya m’Baibulo yokhudza zimene zimachitika munthu akamwalira. Pangani ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Khulupirira Yehova ndi Mtima Wako Wonse”

Miyambo 3 imatitsimikizira kuti Yehova adzatidalitsa tikamamukhulupirira. Kodi mungadziwe bwanji ngati mumakhulupirira Yehova ndi mtima wonse?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Mtima Wako Usapatuke”

Miyambo 7 imafotokoza mmene mnyamata wina anakopedwera ndi zinthu zoipa n’kuchita tchimo chifukwa chonyalanyaza mfundo za Yehova. Kodi ifeyo tingaphunzire chiyani pa zomwe anachitazi?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Nzeru Ndi Yabwino Kuposa Golide

Miyambo 16 imanena kuti ndi bwino kupeza nzeru kusiyana ndi golide. N’chifukwa chiyani nzeru zochokera kwa Mulungu ndi zofunika kwambiri?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Tingachite Kuti Ndemanga Zathu Zizikhala Zabwino

Ndemanga zabwino zimalimbikitsa mpingo komanso zimathandiza anthu omwe amazipereka. Kodi ndemanga yabwino imakhala yotani?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesetsani Kukhala Mwamtendere ndi Ena

Sikuti zimangochitika zokha kuti anthu a Yehova azikhala mwamtendere. Tikhoza kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti tithetse kusamvana komanso kuti tizikhala mwamtendere ndi ena.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Phunzitsa Mwana M’njira Yomuyenerera”

N’chifukwa chiyani kulangiza ana n’kofunika? Miyambo 22 ili ndi malangizo othandiza kwambiri kwa makolo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?

Muzigwiritsa ntchito makadi odziwitsa anthu za jw.org kuti muthandize anthu ambiri kudziwa za Mawu a Mulungu komanso webusaiti yathu.