CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Anapitiriza Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima”: (10 min.)

  • Mac. 4:5-13​—Ngakhale kuti anali “anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba,” Petulo ndi Yohane sanaope kufotokoza zimene ankakhulupirira kwa olamulira, akulu ndi alembi (w08 9/1 15, bokosi; w08 5/15 30 ¶6)

  • Mac. 4:18-20​—Petulo ndi Yohane ananena kuti sangasiye kulalikira ngakhale kuti ankaopsezedwa

  • Mac. 4:23-31​—Akhristu a m’nthawi ya atumwi anadalira mzimu wa Yehova kuti akhale olimba mtima (it-1 128 ¶3)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mac. 4:11​—Kodi Yesu ndi “mwala wofunika kwambiri wapakona” m’njira yotani? (it-1 514 ¶4)

  • Mac. 5:1​—N’chifukwa chiyani Hananiya ndi Safira anagulitsa munda wawo? (w13 3/1 15 ¶4)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 5:27-42

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

 • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Sonyezani zimene mungachite ngati amene mukumulalikira wanena kuti si Mkhristu.

 • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 82

 • Kulalikira ndi Mashelefu Kwathandiza Anthu Ambiri Padziko Lonse: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Onerani vidiyoyi. Ngati mpingo wanu umagwiritsa ntchito kashelefu kapena tebulo, sonyezani mmene mabuku amasanjidwira. Fotokozani dongosolo limene mpingo wanu umatsatira. Ngati nthawi ilipo fotokozani kapena chitani chitsanzo cha zinthu zosangalatsa zimene zinachitika. Kenako fotokozani zimene ofalitsa angachite kuti azilalikira nawo pogwiritsa ntchito njirayi.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 14

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero