Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akumanga Nyumba ya Ufumu ku Australia

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU November 2018

Zimene Tinganene

Zitsanzo za zimene tinganene zokhudza chiyembekezo cha okondedwa athu amene anamwalira.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

Petulo ankafunika kusankha chinthu choti aike pamalo oyamba m’moyo wake. Ankafunika kusankha ntchito yausodzi kapena zinthu zokhudza ufumu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mpingo Wachikhristu Unalandira Mzimu Woyera

Akhristu okwana 3,000 omwe anali atangobatizidwa kumene ankalambira Mulungu mogwirizana ngakhale kuti anali ochokera m’mayiko osiyanasiyana.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri

Kodi ofalitsa a m’mipingo yomwe imalalikira m’gawo la zinenero zambiri angatani kuti azilalikira anthu onse m’gawo lawo popanda kutopetsa eni nyumba?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anapitiriza Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima

Kodi n’chiyani chomwe chinathandiza atumwi kuti azilankhula molimba mtima?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kulalikira ndi Mashelefu Kwathandiza Anthu Ambiri Padziko Lonse

Kodi njira yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri pogwiritsira ntchito kashelefu yathandiza bwanji anthu ambiri?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mpingo Watsopano Wachikhristu Unayesedwa

Ngakhale kuti mpingo wachikhristu unakumana ndi mavuto, unapitirizabe kukula chifukwa chakuti Yehova ankauthandiza.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Muzipereka Mphatso kwa Yehova”

Pali njira zosiyanasiyana zimene tingasankhe kuti tipereke ndalama zathu pothandiza ntchito ya padziko lonse.