KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Anthu ambiri amene amachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu amakhala akufuna kudziwa choonadi chonena za Mulungu. (Yes. 55:6) Choncho, kuti tithe kuwaphunzitsa bwino tiyenera kupitako mobwerezabwereza. Popeza anthu akukumana ndi mavuto osiyanasiyana, njira zimene tingagwiritsire ntchito powathandiza kuti akhalebe ndi chidwi zingakhalenso zosiyanasiyana. Komabe kuti tizipanga maulendo obwereza ogwira mtima, tiyenera kumakonzekera bwino ndiponso tizikhala ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muziyesetsa kupanga ulendo wobwereza mwansanga, mwina pakangodutsa masiku ochepa.​—Mat. 13:19

  • Muzikhala aubwenzi, aulemu ndiponso muzikhala womasuka

  • Muziyamba n’kupereka moni wansangala ndiponso muzimutchula dzina munthuyo. Muzimukumbutsa zimene mwabwerera. Mwachitsanzo mungamuuze kuti mukudzayankha funso, kudzamupatsa magazini, kudzamusonyeza webusaiti yathu, kudzamuonetsa vidiyo kapena kudzamusonyeza mmene timaphunzirira Baibulo. Muzisintha ulaliki wanu ngati munthuyo wasonyeza kuti pali zina zimene zikumudetsa nkhawa.​—Afil. 2:4

  • Muzimuwerengera lemba, kumupatsa buku kapenanso magazini n’cholinga choti muthirire mbewu ya choonadi imene ikumera mumtima mwake. (1 Akor. 3:6) Muziyesetsanso kuchita zinthu zosonyeza kuti mukufuna akhale mnzanu

  • Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira