Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NAHUMU 1–HABAKUKU 3

Khalanibe Maso

Khalanibe Maso

Hab. 1:5, 6

Zinali zosayembekezereka kuti Ababulo angawononge mzinda wa Yuda. Ayuda ankathandizidwa ndi Aiguputo omwe anali amphamvu kwambiri kuposa Ababulo. Kuwonjezera apo, Ayuda ambiri ankaona kuti Yehova sangalole kuti Yerusalemu ndi kachisi ziwonongedwe. Komabe ulosi unkayenera kukwaniritsidwa ndithu ndipo Habakuku ankafunika kukhalabe maso pouyembekezera.

Kodi n’chiyani chikunditsimikizira kuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambiri?

Kodi ndingatani kuti ndikhalebe maso?