Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Khalanibe Maso Pamene Zinthu Zasintha

Khalanibe Maso Pamene Zinthu Zasintha

Zinthu zipitirizabe kusintha, makamaka m’masiku otsiriza ano. (1 Akor. 7:31) Kaya zinthu zimene zasinthazo timaziyembekezera kapena ayi komanso kaya ndi zabwino kapena zoipa, zingathe kusokoneza kulambira kwathu ndiponso ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe maso pamene zinthu zasintha? Onerani vidiyo yakuti Anakhalabe Olimba Mwauzimu Atasamukira Kudera Lina, ndipo kenako yankhani mafunso otsatirawa:

  • Kodi m’bale wina anapereka malangizo otani kwa bambo amene tamuona m’vidiyoyi?

  • Kodi mfundo ya pa Mateyu 7:25 ikugwirizana bwanji ndi zimene zinachitikira banjali?

  • Kodi banjali linachita zotani pokonzekera kusamuka ndipo zimenezi zinawathandiza bwanji?

  • Kodi n’chiyani chinathandiza banjali kuti lizolowerane mosavuta ndi anthu a mumpingo komanso gawo latsopano?

Kodi ndi zinthu ziti zimene zasintha kwambiri pa moyo wanga posachedwapa?

Malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga, kodi ndingagwiritsire ntchito bwanji mfundo zomwe ndaphunzira m’vidiyoyi?