Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akugawira kabuku ka Banja Losangalala ku Georgia

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU November 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Nsanja ya Olonda pophunzitsa choonadi komanso dzina la Mulungu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

‘Yesetsani Kufunafuna Yehova Kuti Mupitirize Kukhala ndi Moyo’

Kodi kufunafuna Yehova kumatanthauza chiyani? Kodi tingaphunzire chiyani kwa Aisiraeli omwe anasiya kufunafuna Yehova?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Kupanga Ulendo Wobwereza

Tiziwathandiza kuti akhalebe ndi chidwi, tizikonzekera bwino ndiponso tizikhala ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muziphunzirapo Kanthu pa Zimene Munalakwitsa

Nkhani ya Yona imasonyeza kuti Yehova satisiya tikalakwitsa zinazake, koma amafuna kuti tiphunzirepo kanthu pa zimene talakwitsazo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Tikuphunzira Kuchokera m’Buku la Yona

Kuganizira zimene zinachitikira Yona kungatithandize kuti tizitha kulimbana ndi zofooketsa, kuti tiziona anthu moyenerera tikakhala mu utumiki komanso kuti tizidalira Mulungu popemphera kwa iye.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?

Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kulambira kwathu ndi mmene timachitira zinthu ndi abale athu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Khalanibe Maso

Zinali zosayembekezereka kuti Ababulo angawononge mzinda wa Yuda. Komabe ulosi unkayenera kukwaniritsidwa ndithu ndipo Habakuku ankafunika kukhalabe maso pouyembekezera.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Khalanibe Maso Pamene Zinthu Zasintha

Zinthu zikasintha zikhoza kusokoneza kulambira kwathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe maso pamene zinthu zasintha?