Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  November 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

NSANJA YA OLONDA

Funso: Kodi mungayankhe bwanji munthu wina atakufunsani kuti kumwamba n’kotani?

Lemba: Yoh. 8:23

Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza zimene Yesu ndiponso Atate ake ananena zokhudza kumwamba.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi mukuona kuti zimene Baibulo linaneneratu palemba ili zikuchitikadi masiku ano?

Lemba: 2 Tim. 3:1-5

Zoona Zake: Popeza kuti ulosi wa m’Baibulo wokhudza masiku otsiriza ukukwaniritsidwa, sitingakayikire kuti ulosi wokhudza zinthu zabwino zimene tikuyembekezera m’tsogolo udzakwaniritsidwanso.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA BAIBULO? (Vidiyo)

Mawu Oyamba: Tikuonetsa anthu vidiyo yomwe imawathandiza kudziwa komwe angapeze mayankho a mafunso ofunika kwambiri. [Onetsani vidiyo.]

Perekani Buku: Bukuli limafotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza zimene Mulungu adzachite pothetsa mavuto a m’dzikoli. [Perekani buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.