Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 27-31

Baibulo Limafotokoza Zimene Mkazi Wabwino Amachita

Baibulo Limafotokoza Zimene Mkazi Wabwino Amachita

M’chaputala 31 cha buku la Miyambo muli malangizo omwe Mfumu Lemueli inapatsidwa ndi mayi ake. Malangizowo anali omuthandiza kudziwa mmene angasankhire mkazi wabwino.

Mkazi wabwino amakhala wodalirika

31:10-12

  • Amakhala wogonjera komabe amafotokoza maganizo othandiza pamene banja likusankha zochita

  • Mwamuna wake amamudalira kuti akhoza kusankha yekha zinthu zina mwanzeru moti sayembekezera kuti azichita kumuuza zoyenera kuchita pa chilichonse

Mkazi wabwino amakhala wakhama ndiponso wanzeru

31:13-27

  • Amagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru ndipo safuna zinthu zapamwamba. Amachita zimenezi n’cholinga choti banja lake lizioneka bwino ndiponso lizikhala ndi chakudya chokwanira

  • Amagwira ntchito mwakhama ndiponso kusamalira banja lake nthawi zonse

Mkazi wabwino amakonda Yehova

31:30

  • Amaopa Mulungu ndiponso amayesetsa kukhala naye pa ubwenzi wolimba